MWAUNGULU, LANJESI NDI CHAZIYA ANYAMUKA MU JULY
Osewera atatu amdziko muno, Patrick Mwaungulu, Lanjesi Nkhoma komanso Lawrence Chaziya, akanika kunyamuka posachedwapa ndipo anyamuka mwezi wa mawa kamba ka zifukwa zina.
Anyamatawa akumana ndi vuto loti omwe amayeza osewera kutimu ya TP Mazembe yaku DRC ali pa tchuthi komanso zipangizo zoyendera zavuta kaye koma mbali zonse zitha pa 10 July 2024.
Yemwe akuyendetsa kuchoka kwa osewerawa kupita kutimuyi, Felix Ngamanya watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati akati apite padakali panopa azikangokhala.
"Kuti osewerawa akayezedwe pamafunika dotolo komanso oyang'ana za mafupa kuti akakhalepo koma tsopano onsewa ali pa tchuthi mpaka pa 10 July nde mpake sitinanyamuke. Takumanso ndi vuto la zitupa zoyendera zomwe zachedwerako nde zonsezi zatiyimitsa kaye." Anatero Ngamanya.
Mgwirizano wapakati pamatimuwa utha ngati osewerawa angakhonze kuyezedwa kwa zachipatala ndipo adzasayina migwirizano yawo kutimuyi. Mwaungulu ndi Nkhoma amasewera FCB Nyasa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores