"ZOMWE TIMANGOMVA ZAKU MULANJE TAZIONA" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya wati timu yake yakanika kupeza chipambano kamba koti zomwe anauzidwa kuti oyimbira amakondera timu ya FOMO waziona yekha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anabwenzetsa nthawi yothaitha kuti masewero athere 1-1 ndipo wati oyimbira anatenga mbali kuti timu ya FOMO izichita bwino mmasewerowa.
"Sindikumvetsa kuti zakhala bwanji kuti masewero athere chonchi chifukwa osewera asewera bwino ndipo anatsatira zomwe tinawauza koma mwina tinabwerera kumbuyo kwambiri nde anzathu amatha kubwera ndi mpira komabe oyimbira amawathandizira mmasewerowa zomwe ndinkangomva kuti zimachitika kuno." Anatero Bunya.
Timu ya Dedza Dynamos ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi awiri (12) pa masewero khumi omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores