"VUTO NDI KUPEZA ZIGOLI BASI" - YASIN
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ikungoyenera kukonza kutsogolo kwawo ngati akufuna ayambe kuchita bwino ndikumapambana masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Mzuzu City Hammers ndipo wati mavuto awo onse wawaona ndipo akonza kuti timuyi iyambirenso kuchita bwino.
"Anali masewero abwino mwina vuto lomwe tilinalo ndi kutsogolo koma ationetsa mbali zomwe tikufunikira kukonza nde tibwerera kuti tikakonze mavutowa." Anatero Yasin.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) pomwe ili ndi mapointsi 6 pa masewero khumi (10) yomwe yasewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores