"ZINAONEKA KU ZOKONZEKERA KUTI TIWINA" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wathokoza anyamata ake kamba kolimbikira kuti apeze chipambano pomwe timuyi imasewera ndi timu ya Civil Service United lamulungu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi zigoli za Christopher Kumwembe ndipo wati kulimbikira kunayambira ku zokonzekera ndipo amadziwa kuti Iwo awina.
"Zinaonekeratu mmene timakonzekera kuti tiwina chifukwa anyamata analimbikira kwambiri ndipo mmasewerowanso tiwathokoze anayikapo mtima mpaka tapeza zigoli zitatu, chipambano ichi ndi chofunikira kwambiri." Anatero Mwase.
Iye wayamikiranso Kumwembe pogoletsa zigoli zitatu mmasewerowa ndipo wati anyamata akamalimbikira amapeza phindu lochuluka poti watola ndalama zambiri.
Manoma tsopano ali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero Khumi (10) omwe yasewera mu ligiyi.
📷: Ark Tembo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores