NYONI WACHIRA KU SILVER
Katswiri wosewera mmbali ku timu ya Silver Strikers, Duncan Nyoni, tsopano wachira pomwe akuyembekezeka kupezeka lolemba likudzali pomwe Silver Strikers ikukumana ndi Mighty Waka Waka Tigers pa bwalo la Kamuzu.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi pomwe amapereka ndandanda wa osewera omwe akadali ovulala kutimuyi lachinayi ndipo wati anyamata atatu ena avulalanso kuonjezera pa ena omwe analipo kale.
Charles Chipala komanso Zebron Kalima sapezeka Kwa masabata awiri kamba kovulala ndipo Tatenda M'balaka sapezekanso sabata ino.
Koma nkhani yabwino ndi yoti Adiel Kaduya ndi Atusaye Nyondo ayamba zokonzekera zawo lachiwiri sabata ya mawa pomwe tsopano achira Malo omwe anavulala.
Silver ili pa nambala yoyamba mu ligi ndi mapointsi 25 pa masewero asanu ndi anayi (9) ndipo ikusiyana ndi yachiwiri mapointsi asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores