"MANOMA ASADZATENGE MIYALA LAMULUNGU" - MALUNGA
Mkulu wa masapota oyimba ku bwalo la zamasewero mdziko muno wa Mighty Mukuru Wanderers, Yonah Malunga, wapempha masapota atimuyi kuti afike pa bwalo la Kamuzu mwaunyinji kuti akaonere timu yawo yomwe ikumenya mwachizungu.
Iye wayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Civil Service United pa bwaloli ndipo wati timu yawo ikapambana poti ili bwino kwambiri komanso masapota asatenge miyala.
"Mkulu wanga Manoma sakupweketsa tikuwina masewero amenewa chifukwa Manoma alibwino kwambiri, masapota abwere adzaone mmene ikumenyera, akumenyatu mwachizungu ndipo asatenge miyala tidzavine, ine Yonah 1 Mpinganjira ndikhalanso konko." Anatero Yonah.
Timu ya Wanderers ili pa nambala yachinayi mu ligi pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi asanu (15) pomwe yapambana kanayi, kufanana mphamvu katatu ndi kugonja kawiri.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr 📷: MH photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores