NKHAKANANGA AKAYIMBIRA COSAFA
Woyimbira wa mdziko muno, Godfrey Nkhakananga, wasankhidwa kuti ayimbire nawo masewero a mpikisano wa chaka chino wa COSAFA Cup womwe uchitikire ku South Africa kuyambira pa 26 June mpaka pa 7 July.
Nkhakananga wasankhidwa mu la oyimbira a mmayiko osiyanasiyana kuti akayimbire mpikisanowu pamodzi ndi Pondamali Tembo yemwe ndi wothandizira kwa oyimbira pomwe ena ndi a mmaiko a Zambia, Zimbabwe, Seychelles, Angola, Mauritius, Botswana, South Africa, Eswatini ndi ena.
Sabata ziwiri zapitazo, Nkhakananga, anakayimbiranso masewero a mpikisano wa World Cup pakati pa ma timu a Djibouti ndi Sierra Leone ku Morocco.
Timu ya dziko lino siyisewera nawo ku mpikisano wa COSAFA kamba koti anatulukamo kuti akulira maliro a Dr Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores