BULLETS YAKANA CECAFA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakana pempho lokasewera mu mpikisano wa CECAFA Kagame Cup kamba koti ali ndi masewero ochuluka kwambiri.
Mkulu woyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, watsimikiza za nkhaniyi kunena kuti atakambirana awona kuti masewero awachulukira nde ndi kwabwino kusamala umoyo wa osewera.
Timuyi ndi imodzi mwa matimu atatu omwe anayitanidwa ndipo TP Mazembe yaku DRC nayo yakana poti osewera ali ku tchuthi pomwe ligi yawo inatha.
Matimu a Simba SC komanso Young Africans athanso osasewera kamba koti alinso ndi masewero ochuluka kwambiri.
Kupatula TNM Supa ligi, Bullets iseweranso mu zikho za FDH Bank, Castel Challenge, Airtel top 8 komanso mu CAF champions league.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores