Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"LERO TIMASEWERA NDI ANTHU 14" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati ngati oyimbira aziyimbira ngati mmene anachitira mmene amakumana ndi Karonga United siziziyenda bwino ndipo wati wawapweteka.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Karonga United pa bwalo la Karonga ndipo wati vuto lomwe lakula ndi loti pali chimene chikusintha akadandaula za oyimbira nde angozitaya.
"Kunena zoona atolankhani mumaona oyimbira athuwa ngati zizitero nde siziziyenda bwino. ziganizo zonse zinali zokondera enawa mwina titha kuti tasewera ndi anthu 14 komabe poti palibe chimene chikumachitika basi tibwerera kwathu." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe yapeza mapointsi 32 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
𝐓𝐡𝐞 𝐒𝐜𝐨𝐫𝐜𝐡𝐞𝐫𝐬 𝐌𝐚𝐤𝐞 𝐇𝐢𝐬𝐭𝐨𝐫𝐲!
🇲🇼 Malawi are the champions 🏆 of the COSAFA for the first time in their history 💥
Zawulendo uno!
owina ndi owina km matimu akuchosana zipumi
"MILANDU YONSE YAMMBUYO ZILANGO ZAKE ZIKUBWERA MMAOLA 48" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi, Fleetwood Haiya, wati matimu onse omwe anaphonya khalidwe mu ligi ya TNM alandira chilango chawo mmaola 48 asanathe pomwe zonse zili mchimake.
Mukalata imene yatuluka ya mtsogoleriyu dzulo yosemphana ndi zimene Moyale Barracks yachitilidwa ku Dedza, iye wati ndi osakondwa ndi mchitidwe umenewu ndipo bungweli lati layamba kale kufufuza.
Iye wati zilango ziperekedwa kwa onse okhudzidwa ndipo wati matimu onse omwe analakwapo mmbuyomu akhale akudziwa chilango chawo mu masiku awiri akudzawa.
Chiyambireni, bungwe la SULOM silinaperekepo chilango chilichonse pa timu kamba ka ziwawa kapena kupanga za chikhulupiliro monga kuthira mkodzo ndi kulowera pa mpanda.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"OSEWERA SANALI BWINO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake sinali bwino mchigawo choyamba zomwe zapangitsa kuti agonje 3-2 ndi timu ya Extreme.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Nankhaka ndipo wati akakonzanso mavuto awo kuti lachitatu akamakumana ndi Kamuzu Barracks adzakonze zonse.
"Sitinasewere bwino mchigawo choyamba pomwe anzathuwa anatichinya koma zimachitika kuti anthu osadzuka bwino mu mpira. Mchigawo chachiwiri titawayankhula zinthu zinasintha, tinasewera bwino mpaka tinapezako zigoli." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe yavutika kuti itolerere mapointsi bwinobwino mmasabata angapo pomwe ili pa nambala 9 ndi mapointsi 32 pa masewero 25.
#KasongaJr
EXTREME YANGOTSALA UMBONI KUTI YATULUKA
Timu ya Extreme tikhonza kutsimikiza kuti ikhala timu yoyamba kusiyana nayo ligi ya chaka chino pomwe phazi lililonse limene Ekwendeni Hammers litasunthe ndekuti chikwanje chiwagwera.
Extreme ili ndi mapointsi 18 kutsatira kugonjetsa Bangwe All Stars 3-2 loweruka ndipo yatsala ndi masewero anayi okha omwe atati apambana onse ndi mapointsi 12. Iyo ikhonza kudzafika pomwe pali Ekwendeni Hammers ndipo kuti isagonjeko komanso Extreme idzamwetse zigoli zodutsira 12.
Mphunzitsi watimuyi, Andrew Bunya, wati kupambana kwawo kwa dzulo ndi kongoonetsa kuti timu yawonso ndi yabwino.
"Tinasewera bwino makamaka mchigawo choyamba pomwe tinapeza chigoli ndipo mchigawo chachiwiri tinaonjezera ziwiri komabe tinatayilira bwenzi tikuti ndi 3-3, tangofuna kuonetsa kuti nafenso sife timu yopanda mphamvu." Anatero Bunya.
"OSEWERA ANAKOMEDWA NDI SAPOTI YA PANJA" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati osewera atimu yake anakomedwa ndi ochemerera nthawi yomwe anapeza chigoli chawo zomwe zinachititsa kuti atayilire.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati mipata yomwe anaipeza akanagoletsa zikanatha kuwachitira ubwino.
"Anali masewero abwino kwambiri tinapeza mipata yoti tikanagoletsa tikanatha kupambana komabe sizinatheke komabe zotsatira izizi zitilimbikitsa. Atapeza chigoli anakomedwa ndi phokoso la ochemerera nde anatayilira." Anatero Mauluka.
Iye wati timu yake sikungoyang'ana zotsala mu ligi koma kuti ithere mu matimu 8 oyamba mu ligi. Iwo ali pa nambala 13 ndi mapointsi 30 pa masewero 26.
"OSEWERA ATHU AWIRI APITA NAWO KU CHIPATALA" - SIMKONDA
Mtsogoleri wa osewera atimu ya Moyale Barracks, Gastin Simkonda, wati timu yawo sinyamuka lero kumapita ku Mzuzu kuti amakonzekere za masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati sangayende bus yawo ili yosweka.
Iye amayankhula izi kutsatira kuphwanyidwa kwa galimoto yomwe amayendera ndi anthu aku Dedza pomwe timuyi inalepherana 1-1 ndi Dedza Dynamos ndipo wati zimenezi si zampira pomwe Chifundo Damba ndi Timothy Nyirenda onse avulazidwa.
"Timalimbikira zokonzekera kuti tizichita bwino komanso pa bwalo la zamasewero timalimbikiranso koma oyimbira akumatisokoneza lero awapatsa penate yabodzanso chabwino tayivomera kenako akutigenda ndi kutiphwanyira bus yathu mpaka anzathu awiri athamanga nawo ku chipatala." Anatero Simkonda.
Iye wati ndi zovuta kuyenda kamba ka mphepo ndi zinthu zina ndipo wati si zampira. Mkulirano unabuka pomwe osewera a Moyale amafuna kumugwira nthupi oyimbira kamba ka penate yomwe anaipatsa Dedza Dyna
"BWALO SILABWINO KOMANSO PANALI MPHEPO YAMBIRI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets wati kuipa kwa bwalo la Rumphi komanso mphepo zimapangitsa kuti timu yake ikanike kusewera bwino pomwe yalepherana 1-1 ndi Ekwendeni Hammers.
Iye amayankhula atatha masewerowa ndipo wati anali masewero ovuta kutengera kuti timu ya Ekwendeni Hammers nayo inachilimika mmasewerowa.
"Choyamba tithokoze Mulungu kuti tapeza zotsatira zimenezi, sanali masewero ophweka ndipo anyamata athu anapeza mipata yoti akanatha kupeza zigoli koma aphonya. Inde bwalo silili bwino komanso mphepo komabe tinawauza anyamata kuti asewerebe." Anatero Munthali.
Timu ya Bullets ikadali pa nambala yachiwiri mu ligiyi pomwe ali ndi mapointsi okwana 44 pa masewero 21 omwe yasewera.
MANOMA AMVEDWA PA MLANDU WAWO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers tsopano yatula nkhawa zawo pomwe loweruka inakumana ndi akuluakulu a bungwe la Football Association of Malawi posagwirizana ndi chigamulo chomwe bungweli linapereka ku timuyi.
Manoma anatsogozedwa ndi a Kalekeni Kaphale ndipo anaperekezedwa ndi David Kanyenda, Chancy Gondwe, Limbani Magomero, Roosevelt Mpinganjira, Chimwemwe Kaonga, mphunzitsi Mark Harrison komanso Stanley Sanudi.
Kaphale wati FAM inalakwitsa posaitana Wanderers popanga zinthu zawo zomwe ndi zotsutsana ndi FIFA, malamulo a Airtel Top 8 sangapose malamulo a FIFA oti chiganizo cha oyimbira ndi chotsiriza komanso kuti manambala a mipando anachoka bwanji pa 70 kufika 239.
Iye wati bungweli lichotse chilango chomwe inapereka kwa Wanderers. Williams Banda, Raphael Humba, Alfred Gunda ndi Gomegzani Zakazaka ndi omwe amayankhapo ku FAM ndipo Allison M'bang'ombe ndi yemwe amatsogolera mkumanowu pomwe okumva milandu, Khumbo Soko ndi Ted Roka anali pomponso.
Chiga
"ULENDO UNO WOKHA MULUNGU ALINAFE TITENGA COSAFA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati nsi wokondwa kamba koti timu yawo yafika mu ndime yotsiriza ya chikho cha COSAFA ndipo wati ulendo uno ayesetsa kuti agonjetse Zambia.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Mozambique 2-1 mu ndime ya matimu anayi kuti afike mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu. Iye wati sakuyiopa Zambia ndipo lamulungu akungofuna chikho basi.
"Zambia ndi masewero ovutanso koma Pali zifukwa zimene amatigonjetsera mmbuyomu koma panopa mbiri singagwirenso apapa Zambia ikagwira magobo kuti itigonjetse koma Mulungu ali mbali yathu titenga chinthuchi." Anatero Fazili.
Malawi inatsalira ndi Mozambique kudzera mwa chigoli cha Lonica Tsanwane koma Temwa Chawinga anapeza zigoli ziwiri kuti ipambane. Masewero ndi Zambia achitika lamulungu.
Mighty mukuru kwiman kwambir kt aneba asatimvutitse
Bbb
Kuno ekwenden 1 inayo 1
Bules lelo zivuta
Isaias
"CHIYAMBIRENI LIGI TAMENYAKO NDI TIMU YANZERU" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve, Enos Chatama, wati timu yake yasewera masewero ovuta kwambiri chiyambireni mu ligi ya chaka chino pomwe wayamikira FOMO FC kuti ndi timu yabwino.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timu yake yapambana 2-1 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati nsi okondwa poti afika mu ndime ya matimu asanu ndi atatu ndipo maso ake azikonza za ndime imeneyi.
"Anali masewero ovuta kwambiri mwina tasewera masewero ambiri oti ena tinagonja koma lero tasewera ndi timu yabwino, tiwayamikire FOMO yamenya bwino makamaka mchigawo choyamba pomwe anatipanikizadi koma mchigawo chachiwiri nde tamenya. Ali ndi mphunzitsi wabwino ndipo tamenya ndi timu yoti ikudziwa chimene ikupanga." Anatero Chatama.
Mphunzitsiyu anati timu yake yaphonya kwambiri koma nzosadandaulitsa poti yatenga mapointsi omwe atsimikizira malo awo mu ndime Ina. Timuyi ili pa nambala yoyamba ndi mapointsi 36 pa masewero 18.
Wolemba: Hast
"OYIMBIRA NDI YEMWE WATIPWETEKA" - SOSTEN
Wapampando wa timu ya FOMO FC, Hadweck Sosten, wati timu yake yagonja chifukwa choti oyimbira, Mayamiko Kanjere, amakondera timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Kanjere akumudziwa kale kuti sayimbira bwino.
"Anali masewero abwino, tamenya bwino kwambiri muone timasunga mpira kwambiri kuposa iwowa timawamenya koma oyimbira ziganizo zake sizinali bwino. Anawapatsa penate yabodza pomwe iwo akagwira samayimba nde iyeyu watipweteka." Anatero Sosten.
Iye watinso timuyi ilowa mu Supa ligi ya chaka cha mawa. Kutsatira kugonjaku, timu ya FOMO ikadali pa nambala yachiwiri mu gulu B ndi mapointsi 33 pa masewero 18.
"OSEWERA TAGWIRIZANA KUTI TITENGE COSAFA" - CHAWINGA
Mtsogoleri wa timu ya Scorchers ku mpikisano wa COSAFA Women's Championship, Temwa Chawinga, wati iye ndi timu yake agwirizana kuti chaka chino chokha atengeko chikhochi koyamba mu mbiri ya mpira.
Chawinga amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Mozambique mu ndime ya matimu anayi a chikhochi lachisanu ndipo wati timu yawo ndi yokonzeka kupanga chilichonse kuti akhale ukatswiri.
"Zokonzekera zikuyenda bwino atsikana tonse mu camp molalo ili pa mwamba pomwe tikupita mmasewerowa. Tinayamba kusewera mpikisanowu ndi kalekale ndipo tagwirizana kuti mwina chaka chino titengeko." Anatero Chawinga.
Iye anatinso masewero awo ndi Mozambique akhala ovuta potengera kuti matimu ambiri abwera mwa mphamvu ndipo samayembekezera timuyi kufika mu ndimeyi nde chizolowezi choti amayigonjetsa sichigwira.
Malawi ikumana ndi Mozambique mawa pomwe akufuna kufika ndime yotsiriza kachiwiri mu zaka zitatu. Matimu a Zambia ndi Zimbabwe akumananso mma
FAM IWUNIKIRA MLANDU WA WANDERERS LOWERUKA
Bungwe la Football Association of Malawi lati likhala likuunikiranso dandaulo la timu ya Mighty Mukuru Wanderers loweruka lapa 14 October 2023 kuti imvetse zina mwa zomwe inadandaula.
Wofalitsa nkhani za bungweli, Gomegzani Zakazaka, watsimikiza kuti komiti yoona zokhazikitsa bata ku bungweli, ikhala ndi mkumano omwe aone pa madandaulo a timuyi.
Izi zikudza pomwe Wanderers inalembera bungweli kudandaula pa chigamulo chimene analandira kamba kopanga zachisokonezo pa masewero amu Airtel Top 8 ndi Silver Strikers ndipo anauzidwa kuti apereke K24.5 million.
Akuluakulu a Wanderers sanakhutire ndi chigamulochi ndipo analembera FAM pa zinthu zodutsira zisanu zomwe zinalakwika.
Photo credit: Ark Tembo #Tawonga2023
Patson kalimbuka
CHAWINGA WAGOLETSANSO NDI MANCHESTER UNITED
Katswiri wa Scorchers, Tabitha Chawinga, wapereka mwayi waukulu kutimu yake kuti ipitilire mu mpikisano wa UEFA Champions League pomwe dzulo anagoletsa chigoli cha PSG pomwe alepherana 1-1 ndi Manchester United.
Chawinga anatsogoza timu yake pa mphindi 64 za masewerowa koma Melvin Meladi yemwe anachokera panja wa Manchester United anabwenza kuti masewero athere 1-1.
Iye anasewera kwa mphindi 88 asanamutulutse ndipo awa anali masewero ake oyamba mu chikhochi. Matimuwa akumananso mu masewero achibwereza sabata yamawa lachitatu ku France ndipo owina adzafika mu ndime ya mmagulu ku mpikisanowu.
Chawinga wakhala wosewera oyamba wa mpira wamiyendo wa amayi ku Malawi kusewera mu UEFA Champions League komanso kugoletsa.
Good work
"MWINA AMAPHWEKETSA TIGERS POTI TINAIMITSA WANDERERS" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati ndi wokhumudwa kwambiri ndi mmene timu yake inasewera lachitatu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati waonera mpira woipa chiyambireni ku timuyi.
Iye wayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Tigers ndipo wati mwina kuiderera Tigers ndi kumene kwawapweteketsa poti amachoka koimitsa Wanderers.
"Sitinasewere bwino ndipo sindinasangalatsidwe, mwina anatayilira poti anasewera bwino ndi Wanderers koma kaseweredwe akaka ndi koipitsitsa komwe ine ndaonako, ndakhumudwa kwambiri, zimachitika koma osati ndi zigoli zonsezi." Anatero Chingoka.
Iye wati akonza mavuto awo kuti akamakumana ndi Bullets adzachite bwino ndipo osewera awo ovulala awagwiragwiranso kuti adzapezeke. Moyale ili pa nambala 12 ndi mapointsi 30 pa masewero 25.
Semi finals cosafa women
Malawi vs Mozambique Zambia vs Zimbabwe | Botswana
"THEY SCORED TWO, WE CAN SCORE 10 GOALS IN BLANTYRE" - CHIDATI
Civo United Vice Coach, Wilson Chidati, says his team is not yet out of the Airtel Top 8 despite having a 2-0 home loss against FCB Nyasa Big Bullets and says there's no algebra in Football.
Chidati said this after the match at the Civo Stadium and downplayed fears that they will be knocked out in the tournament and said the 90 minutes in Blantyre will confirm that.
"There's no algebra in Football, anything can happen. They have scored two goals here and we can score ten goals in Blantyre." Said Chidati.
The Civil Servants are hit with poor strings of results as they are also in danger of getting relegated from the TNM Super league.
"WE TRUST EVERY PLAYER WE SIGNED" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says he puts trust on each player he signed and this helps the squad to perform even if it is rotated.
The Zimbabwean said this after the team picking a 2-0 away win in the Airtel Top 8 first leg against Civo United and was to responding to how he changed the team in the match.
"The story is about not being afraid to field the players we registered. We need each and every player to be prepared, we talked this when we were playing friendlies, I kept on changing the line up but people were complaining."
"We were preparing for this, this season we have a lot of games, we play 3-4 games in 10 days and other games are played on hard surfaces so we need to manage the squad." Said Pasuwa.
Maxwell Gasten Phodo and Hassan Kajoke got the goals to set Bullets in a safe place to sail through to the Semi finals ahead of the second leg in Blantyre.
"SITIKUYIMIKA MANJA MMWAMBA MONGA RED LIONS" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu ya Red Lions iyesabe mmasewero awo omwe atsala kuti imenyere nkhondo yosatuluka mu ligi pomwe wati iwo sanatuluke.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Balaka ndi Kamuzu Barracks ndipo wati kuchinyitsa mwachangu ndi komwe kunawapweteketsa koma ayesetsa mmasewero omwe yatsala nawo.
"Tivomereze kuti tatayadi mapointsi, sitinasewere monga mwa plan yathu mwina zigoli tinachinyitsa koyambilira zinatibalalitsa tivomereze kuti taluza. Masewero akadalipo, sitikufooka mmasewero omwe atsalawo tiyesetsa kuti tiwine." Anatero Masapula.
Timu ya Red Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero okwana 25 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
"TIKUFUNA TIKWERE MU LIGI" - CHIRWA.
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati masewero atimuyi ndi Red Lions anali ofunikira kwambiri pomwe akuyang'ana kuti athere pa nambala yabwino mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Red Lions 2-0 pa bwalo la Balaka ndipo wauza ochemerera atimuyi kuti iwo agwira ntchito yotamandika.
"Anali masewero ofunikira kwambiri kuti tikwere mu ligi nde 2-0 kupambana ndine okondwa kwambiri. Masapota akhalebe nafe, ife tiyesetsa kuti tigwire ntchito ndipo timaliza pa bwino ndithu." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks tsopano yasuzumira ku matimu anayi oyamba mu ligiyi pomwe ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 39 pa masewero 25 omwe yasewera.
"TINAWAUZA ANYAMATA KUTI AKAFERE MU BWALO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati ndi wokondwa ndi mmene timu yake inasewera ndi Moyale Barracks pomwe wati masewerowa amaonetsa tsogolo la timuyi mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Moyale Barracks 3-0 pa bwalo la Kamuzu koma wati akufunikirabe kupambana mmasewero omwe atsala nawo kuti athere pabwino.
"Anali masewero ofunikira kwambiri potengera kuti amationetsa tsogolo lokhala mu ligi nde ndithokoze anyamata analimbikira kuchinya Moyale 3-0 si zophweka koma zatengera kulimbikira kwawo. Apapa ntchito ikadalipo chifukwa ligiyi yavuta kwambiri." Anatero Nyambose.
Iye anatinso kutsogola masewero omwe asewera kulibe ntchito koma kumapambana poti Fodya umanena wapamphuno. Tigers ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi 31 pa masewero 26.
GHEDO LORENZO WAPAMBANA MPHOTO YOSEWERA BWINO PA MWEZI
Timu ya Chitipa United yasankha katswiri wawo womwetsa zigoli, Ghedo Lorenzo, kuti wapambana mphoto ya osewera bwino wa mwezi wa September atapeza mavoti ochuluka kuposa anzake awiri.
Timuyi yalengeza izi lachitatu madzulo kudzera pa tsamba lawo pomwe iye waposa Ramadhan Ntafu ndi Stain Patrick pa mphotoyi.
Iye anagoletsa Chigoli chokhacho pomwe timuyi inagonja 2-1 ndi Chitipa United komanso chimodzi pomwe anagonjetsa timu ya Bangwe All Stars 2-0 ku Blantyre.
Iye atenga ndalama zokwana K100,000 kamba kopambana mphotoyi. Osewera monga George Chikooka Rajab Nyirenda ndi Blessings Joseph apambanakonso mphotoyi.
"SI IFE OKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu yake siyokhutira ndi kufanana mphamvu ndi Silver Strikers pomwe amafunikira chipambano ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 pa Chitowe ndipo wati akonza mavuto awo pomwe akukakunana ndi timu ya Karonga pa bwalo lamulungu likudzali.
"Sife okhutira ndi zotsatirazi, timayenera kupambana chifukwa ndi mmene ligi yavutiramu mapointsi atatu ndi ofunikira koma tatenga imodzi basi tingovomereza." Anatero Mwansa.
Iye wati masewero awo ndi Karonga akhala ovuta kamba koti akakumananso ndi timu yabwino koma ayesetsa kukonza mavuto awo ngati kuphonya Kwambiri kuti akapambane masewerowa.
Timu ya MAFCO ili pa nambala 9 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 32 pa masewero 25 ndipo yatsala ndi masewero asanu kuti amalize mu ligi ya TNM.
"NGATI OSEWERA AKUFUNA NDALAMA AZIWINA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake yataya mapointsi pa masewero omwe akanatha kupambana ndipo wati ngati osewera awo akufuna ndalama azipeza zigoli.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi MAFCO ku Chitowe ndipo wati timu yake yataya mipata yochuluka yomwe akanatha kupambana mmasewerowa.
"Tafanana mphamvu ndi MAFCO pa masewero omwe tikanatha kupambana, tinasewera bwino mphindi zonse koma tinakanika kupeza zigoli nde ngati sikugoletsa ndekuti mufanana mphamvu ngati simunachinyitsenso." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachinayi pomwe ili ndi mapointsi okwana 40 pa masewero 23 omwe yasewera. Lolemba, iwo akumana ndi Mighty Mukuru Wanderers.
Mafco vs silver
mwmtgatm
Give ur predict all games on tnm as castel cup
Semi finals
Links
WANDERERS YACHOTSA STEVE PALAMEZA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yalengeza kuti yasiyana ndi mmodzi mwa akuluakulu kutimuyi, Steve Palameza, atamupeza olakwa pa milandu Ina yosowa khalidwe kutimuyi.
Mu kalata yomwe timuyi yapereka kwa Palameza, yamuuza kuti amuchotsa kamba ka milandu itatu yomwe anavomera kuti ndi olakwa pa 19 September 2023, akuluakulu ena oona zakhalidwe atamuitana.
Mmalipoti ena, zamveka kuti iye ndi amene anasowetsa K60 million ku timuyi pomwe amakatenga ngongole mu dzina la timuyi.
Source: Times
Ndidzoona ásowe
MWAUNGULU WAYAKA MOTO
Osewera wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Patrick Mwaungulu wasankhidwa mu timu ya osewera 11 omwe asewera bwino mu sabata yangothayi ndi tsamba la Africa Soccer Zone.
Izi zadza kamba kosewera bwino mmasewero omwe Bullets inaswa MAFCO 3-0 kuti atenge chikho cha FDH Bank lamulungu.
Mmasewerowa, Mwaungulu anathandizira zigoli ziwiri za masewerowa.
Mwaungulu is best prayer number one
MALAWI YAMALIZA BWINO MU GULU A
Timu ya Scorchers yapanga mbiri yapaderadera pomwe yapambana masewero awo onse amugulu pomwe apambana 3-1 kugonjetsa timu ya Madagascar masana a lachiwiri ku South Africa.
Vanessa Chikupira anatsogoza Malawi pa mphindi 22 asanabwere Leticia Chinyamula pa mphindi 24 koma Madagascar inabwenza chimodzi pa penate ndipo Asimenye Simwaka anagoletsa chigoli chapamwamba kuti timuyi itsogole 3-1 pa mphindi 38.
Mmasewerowa, osewera akuluakulu ngati Temwa Chawinga, Chimwemwe Madise ndi Madyina Ngulube sanalowe. Mmasewero ena, timu ya South Africa yagonjetsa timu ya Eswatini 3-0 kuti imalize pachiwiri.
Malawi yafika mu ndime ya matimu anayi ndipo Zambia ndi Mozambique afikanso mu ndimeyi pomwe amu gulu C sanadziwike.
BREAKING: Ex-Chelsea winger Eden Hazard has announced his retirement from football after leaving Real Madrid at the end of last season.
Hazard won the Premier League, Europa League and La Liga during his 16-year career where he represented Lille, Chelsea and Real Madrid and was capped 126 times by Belgium.
GABA, PAPA JR AND MZAVA VISIT SCORCHERS
Famous Malawian Footballers, Gabadinho Mhango, Gerald Phiri Jr and Limbikani Mzava, visited the Malawi Women's Football team as part of motivating the team to win the COSAFA Women's Championship.
The trio made this ahead of the team's match against Madagascar in their Group A final match this afternoon and told them to play with their hearts to win the tournament.
The team has qualified for the Semi finals of the tournament after securing victories over South Africa and Eswatini and are favourites to win this year's tournament.
Photo credit: Times
CHAWINGA'S PSG FACE MANCHESTER UNITED TODAY
Scorchers captain, Tabitha Chawinga, will become the first Malawian female Footballer to play in the UEFA champions league as her team PSG play Manchester United today.
Chawinga made her debut last week when her team lost 1-0 to Champions, Olympic Lyonnaise and got her debut goal in a 1-0 win over Saint-Ettiene in the league.
A game against Manchester United will be her third at the team and her first ever Champions League match. The match will be played at the Leigh Sports Village from 21:00hrs to night.
Achina Maguire aakazi
"OSEWERA ACHISODZERA APATSIDWA MPATA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati osewera achisodzera omwe anapita ndi timuyi apeza mpata osewera pomwe timuyi ikumane ndi Madagascar mu masewero omaliza a gulu A.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake sikudelera komanso ikufunitsitsa kuti imalize ndi zipambano zitatu mu gulu mwawo.
Iye wati mmasewerowa apereka mpata kwa osewera achisodzera kuti aziphunzirako kwa akuluakulu ndikuti timuyi ikhalebe ya mphamvu mpaka kale.
"Tikuyembekeza masewero abwino, Madagascar ndi timu yabwino ndipo itha kutidzidzimutsa komabe tikufuna kupambana masewerowa. Osewera achisodzera asewera mawa kuti achotseko mantha." Anatero Fazili.
Timu ya Scorchers inafika kale mu ndime ya matimu anayi pomwe inagonjetsa South Africa ndi Eswatini mu gululi.
1~1
Games