Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TIVOMEREZE KUTI LERO SITINALI BWINO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu yake sinasewere bwino mmasewero awo a ndime yotsiriza ya FDH Bank Cup mpake akanika kutenga ukatswiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo iye wavomereza za kugonja kwawo mmasewerowa.
"Ife tagonja, sitinachite bwino ndivomereze ngati mphunzitsi kuti zinthu zativuta kuyambirira timakanika kumaka nde anzathuwa anatengerapo mwayi ndi kutichinya nde tiwayamikire poti apambana." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yathera pa nambala yachiwiri ya mpikisanowu pomwe Bullets yamaliza poyamba ndipo yatenga K30 million.
#Tawonga2023
"ZA FDH TAYIWALA TIKUYANG'ANA ZIKHO ZINA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wayamikira anyamata ake kamba kosewera bwino mpaka kutetezanso chikho cha FDH Bank masana a lamulungu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anapha MAFCO 3-0 kuti atenge chikhochi koma iye wati maso awo tsopano aika pa zikho zina tsopano.
"Mmene zateremu ndekuti za FDH zatha apa tikuyang'anani masewero omwe akubwera kutsogoloku, inde alipo ambiri nde tiyamba kukonzekera mawa ndipo anyamata onse akonzekere kugwira ntchito." Anatero Munthali.
Timuyi yalandira ndalama zokwana K30 million kamba kokhala akatswiri a mpikisanowu omwe tsopano awutenga kachiwiri motsatana.
"TIMU IKAGONJA SIKUTI IZINGOGONJABE" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wadzudzula mchitidwe wa anthu omwe akumayankhula kwambiri timuyi ikapanda kuchita bwino pomwe wati mu mpira matimu amaluzanso.
Iye amayankhula izi atagonjetsa timu ya Blue Eagles 2-1 pa bwalo la Dedza ndipo wati masewero awo anali ovuta koma chipambano chinali chofunika potseka pakamwa anthu oyankhula kwambiri.
"Vuto lake anthu amayankhula kwambiri, ineyo ndamenyapo mpira, nthawi zonse sikuti mukaluza ndekuti ndinu oluza basi nde komabe anyamata anaikapo mtima lero kuchokera kumbuyo mpaka tapambana." Anatero Chirwa.
Chipambano cha timuyi chaitengera pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ali ndi mapointsi 34 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi.
"NGAKHALE DEDZA YACHITA KUTI TINAKUMANA NAZO" - KANANJI.
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inasewera bwino kwambiri koma zavuta ndi kukanika kugoletsa ndi chifukwa chake agonja masewero awo 2-1 ndi Dedza Dynamos.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa ndipo wati timu yake ndi imene inasewera bwino kuposa Dedza Dynamos koma chibwana cha osewera chawapweteketsa.
"Anali masewero abwino kwambiri anyamata analimbikira koma tizibwana pang'ono ta anyamatawa ndi timene tatipweteketsa, anzathuwa anangobwera ndi kutichinya koma tinawapanikiza ndithu ndipo akuchita kunena okha kuti lero anakumana nazo." Anatero Kananji.
Iye wati kutaya mapointsi kukupereka ntchito yaikulu koma mavuto awo awakonza. Blue Eagles ikadali pa nambala 10 ndi mapointsi 30 pa masewero 25 omwe yasewera.
"WE NEED TO BEAT SILVER NEXT WEEK. SIMPLE" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, was left with disappointment on Sunday after his team failed to claim maximum points after conceding a late goal to draw 1-1 against Moyale Barracks at the Kamuzu Stadium.
The Englishman said after the game that his side is missing a lot of chances and that the points that are dropping now, will be remembered at the end of the season.
"At the end of the season we will be looking back at these points dropped, this one, against Extreme in the first round, Chitipa here, I mean we will remember these points. I am very disappointed, to move on simple, we have to beat Silver in Lilongwe, no option." Said Harrison.
The Nomads are still top of the table after collecting 47 points from 24 points and are four points ahead of FCB Nyasa Big Bullets who have three games in hand.
"KUMBUYO KWA WANDERERS SAMAYENDA NDE TINAPEZA MPATA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati kufanana mphamvu koyenda ndi timu ya Wanderers ndi zonyaditsa ndipo ziwathandizira pa nkhondo yawo yotsala mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anapeza chigoli mu mphindi zakumapeto kuti afanane mphamvu 1-1 ndipo wati anayiona Wanderers chofooka chomwe osewera ake anagwiritsa ntchito.
"Ndinayiona kuti Wanderers sikuyenda kumbuyo kwawo nde ndinawauza osewera kuti ayipanikizebe mchigawo chawo chomwecho mpaka zinatheka kuti tapeza chigoli chomwe ndi chofunikira kwambiri." Anatero Chingoka.
Moyale tsopano izipita mmasewero awo ndi Mighty Wakawaka Tigers lachitatuli ili pa nambala 11 ndi mapointsi 30 pa masewero 24.
Results
Portugal
Seginda liga results
Respect to tip mazembe fc becz bb learn something
Big bullets 3-0 mafico
FDH BANK CUP FINALS NYASA BIG BULLETS VS MOYALE BALACKS
Ife nde ndima gunners mancity samala
Newcastle
Nselema siyahamba
Karonga v Ekwendeni hammers
MAULE
"MATIMU AKUBWERA KUTSOGOLOKU AKONZE KUMBUYO KWAWO" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati timu yake ili ndi mwayi ochuluka oti atenge chikho cha COSAFA Women's Championship kamba ka mmene akugoletsera zigoli ndipo wati matimu ayembekezere kuzisamba.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Eswatini 8-0 kuti afike mu ndime ya matimu anayi ya mpikisanowu ngakhale kuti masewero amodzi sanasewere. Iye wati atenga chinthuchi.
"Malingana ndi mmene tikusewerera ndi kugoletsera zigoli chikho tithadi kutenga chifukwa kumbuyo mwina titha kumavutika koma mwayi wake tikumachinya nde ena akubwerawa akonze kumbuyo kwawo." Anatero Fazili.
Timuyi ikutsogolera mu gulu A ya mpikisanowu pomwe ili ndi mapointsi 6 pa masewero awiri ndipo yakwanitsa kumwetsa zigoli 12.
"TIKANAWINA KOMA OYIMBIRAWA SANAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, anachoka atakwiya pa bwalo la Mpira loweruka pomwe wati oyimbira amapanga ziganizo zofuna kuyipweteka timu yake pomwe imasewera ndi Bangwe All Stars.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe anafanana mphamvu 1-1 ndi zigoli za Levison Maganizo komanso James Tambwali ndipo wati kukonza kwawo kunali kuti apambane basi.
"Anali masewero ophweka kwambiri koma oyimbira amafuna kuti tizilimbana. Nokha mukuona chinthu akakukanirani molalo imatha nde timangokhala kumbuyo kuja poopa kuti awapatsa chigoli mwina cha offside." Anatero Chirwa.
Iye wati sanakhutire ndi zotsatirazi pomwe wati anakonza kuti apambane. KB ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 36 pa masewero 24.
"ANYAMATA AKUPHONYA KWAMBIRI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake ikuchulutsa mipata yomwe akuphonya kwambiri zomwe zikupangitsa kuti azitaya mapointsi ambiri mmasewero awo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anafanana mphamvu ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Mpira ndipo wati anyamata ake sakudekha akafika pagolo.
"Anali masewero ovuta kwambiri, anzathuwa anasewera mchigawo choyamba pomwe ife mchigawo chachiwiri koma kungoti mipata yathu taphonya kwambiri, anyamatawa sakumadekha akafika pagolo." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe yapeza mapointsi okwana 32 pa masewero 24 omwe yasewera.
Well done
Live football today
"TAKONZA MAVUTO ATHU OMWE TINAPANGA NDI BULLETS" - KAMWENDO
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati timu yawo yaunikira bwino mavuto omwe anali nawo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets mkati mwa sabatayi ndipo abwera mosinthika pokumana ndi Kamuzu Barracks loweruka.
Kamwendo amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwa pa bwalo la Mpira ndipo wati ngakhale nthawi yokonzekera inali yochepa, iwo akwanitsa kuwauza anyamata zoyenerera.
"Tinasewera bwino ndi Bullets mwina tinachita kuwapatsa chigoli koma zonse zinali bwino vuto linali kuphonya kwambiri nde takonza zonsezo. Nthawi inali yochepa koma ntchito yake sinali yovuta ngati amakwanitsa kuyandikira golo, ziganizo ndi zomwe zimavuta, pomenya pagolo amapatsira, popatsira amamenya nde takonza." Anatero Kamwendo.
Bangwe ili pa nambala 8 pomwe ili ndi mapointsi 31 pa masewero 23 omwe yasewera.
Kod final ya Nyasa big vs mafco liti?
Iliko mawa pa 8 October.
"TAYENDA KWAMBIRI NDE TINALI TISANAMASUKE" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake inavutika kwambiri mchigawo choyamba ndi timu ya Bangwe All Stars kamba koti ulendo wawo waku DRC unali utawamanya osewera matupi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 ndipo anati kukonzekera kwawo sikunali kwa nthawi zonse koma wathokoza osewera atimuyi kamba kolimbikira ndi kupeza chipambano.
"Choyamba tithokoze osewera athu kamba ka chipambanochi, anali masewero ovuta kwambiri poti tikuchokera ku DRC nde tafika lamulungu anyamata sanapange zokonzekera bwinobwino nde matupi anali omangika koma mchigawo chachiwiri tasewera bwino mpaka tinapeza chigoli." Anatero Munthali.
Timuyi tsopano yabwera pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 43 pa masewero 20 omwe yasewera mu ligiyi.
870667416
"NZOVUTA KUFOTOKOZA, TAGONJA MOPWETEKA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake yagonja mmasewero awo omwe amatsogola 2-0 ndi Red Lions kamba koti anyamata ake anatayilira Poona kuti apambana kale.
Kajawa amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-2 pomwe anagoletsetsa zigoli zitatu mu mphindi zisanu zakumapeto ndipo wati ndi zinthu zovuta kuzimvetsetsa.
"Ndi Zovuta kufotokoza, tagonja tikutsogola 2-0 mpaka anzathu anabweramo, mwina anyamata anatayilira poyesa kuti apambana masewerowa koma zimangofunika kuti tingomalizitsa mpirawu sindikudziwa kuti chachitika ndi chani koma ndi mmene mpira umakhalira." Anatero Kajawa.
Kutsatira kugonjaku, Karonga ikhalabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi pomwe ili ndi mapointsi 33 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi.
"RED LIONS SITULUKA MU LIGIYI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati chipambano chomwe apeza ku Karonga lachitatu ndi chokoma kwambiri ndipo chawalimbitsa mtima kuti satuluka mu ligi ya chaka chino.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe yagonjetsa Karonga United 3-2 pomwe inamwetsa zigoli zitatu mu mphindi zisanu zakumapeto kuti apeze chipambanochi. Iye watsindika kuti sakutuluka.
"Tithokoze anyamata kuti anaikirapo mtima ndipo ena omwe anachokera panja sanataye mtima, mutha kuona anzathu anapeza zigoli zawo komabe ife tiwalimbirabe. Red Lions chaka chino sikutuluka, apa tafika 21 tikapambana Ina tikhala tikusunthabe." Anatero Masapula.
Chipambanochi changosintha mapointsi pomwe tsopano ili ndi 21 pa masewero 24 omwe yasewera chaka chino koma ikadalibe pa nambala 15 mu ligiyi.
"SITILI PA MTENDERE NDIPO TIKUFUNIKA KUCHILIMIKA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati ndi wokondwa kwambiri kamba koti timu yake yapeza chipambano pomwe amasewera ndi Civo United koma wati sizikutanthauza kuti ali pa mtendere.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 1-0 pa bwalo la Rumphi ndipo wati samayembekezera kuti timuyi ingasewere bwino motero.
"Ndine wosangalala kwambiri Chimwemwe chodzadza tsaya komanso ndiwanyadire osewera athu sindimayembekezera kuti tingapambane poti anyamata ambiri ndi ovulala koma asewera bwino. Tichilimikabe chifukwa ligi yavuta nde pakufunika osamataya mapointsi." Anatero Chingoka.
Moyale tsopano yafika pa nambala 11 pomwe yatolera mapointsi 29 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
"TIGWIRITSA NTCHITO MASEWERO APAKHOMO BASI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake tsopano iyang'ana pa masewero anayi omwe yatsala nawo apakhomo kuti itsale mu ligi pomwe yatsakamira ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Moyale Barracks ku Rumphi ndipo wati masewero apakhomo atsala nawo ambiri kusiyana ndi koyenda nde angolimbikira pakhomopo.
"Sikuti zinali zoyipa tikumapeza mipata koma tikuphonya kwambiri. Tatsala ndi masewero awiri koyenda ndipo ena onse ali pa khomo, tingogwiritsa ntchito mwayi osewerera pakhomopo kuti mwina titsale mu ligi." Anatero Chidati.
Civo yatsakamira pa nambala 14 mu ligi pomwe yatolera mapointsi okwana 25 pa masewero 24 omwe iyo yasewera mu ligiyi.
"CHIGOLI TANGOWAPATSA KUTI ENI CHINYANI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati masewero omwe timu yake yagonja 1-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu ndi opweteka kwambiri kamba koti chigoli chake angopereka.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri koma aphonya mipata kamba kosowekera kudekha akafika malo oti atha kugoletsa.
"Zopweteka kwambiri, Bullets ndi timu yaikulu koma tinakwanitsa kuyisunga bwinobwino kungoti chigoli tangowapanga kuti eni chinyani. Tinapezadi mipata yabwino koma anyamata athu Sanathe kumenya bwino kuti agoletse." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe tsopano ili ndi 31 pointsi mu ligi ya TNM pomwe ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
"MAFCO TSOPANO ILI BWINO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO FC, Pritchard Mwansa, wayamikira osewera atimuyi kamba ka kuzipereka kwawo kuti kukuthandiza timuyi kuchita bwino kwambiri mmasewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 ndi Ekwendeni Hammers ndipo wati tsopano timu ya MAFCO ili bwino kwambiri.
"Ndife wosangalala kamba ka chipambanochi, anali masewero ofunikira kwambiri poti ligi yavuta pa log table koma anyamata akuchita bwino, mmasewero 5 apitawa tachita bwino mwina ndi mmene ligi ilili sizophweka kupambana masewero 4-5 nde tiwathokoze." Mwansa anafotokoza.
Timuyi yachoka pa nambala 12 ndipo yafika pa nambala 8 ndi mapointsi 31 pa masewero 24 omwe iyo yasewera mu ligiyi.
"CHIBWANA NDI CHIMENE CHIKUMATIPWETEKA" - NYONI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati timu yake yagonja masewero ake ndi MAFCO mu ligi kamba ka chibwana pomwe wati akuphonya mipata kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndipo wati chibwana cha osewera akafika ku golo la anzawo, akumalangika nacho ku golo kwawo.
"Anali masewero abwino tinapeza mipata yoti tikanatha kupeza zigoli koma tinaphonya nde mukakumana ndi timu yoti ikufuna zigoli imakulanga kumapeto, mwina tizibwana pang'ono koma anyamata asewera bwino." Anatero Nyoni.
Sizikuyendabe ku Ekwendeni pomwe yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 29 pa masewero 25 omwe yasewera mu ligiyi.
mighty mukuru wandaras
MPONDA WATSOGOLERA LEOPARDS KU CHIPAMBANO CHINA
Katswiri wakale watimu ya Flames, Peter Mponda akuchita bwino ngati mphunzitsi tsopano kutimu ya Black Leopards pomwe wayitsogolera ku chipambano chachiwiri mu ligi ya Motsepe Foundation Championship ku South Africa.
Leopards yagonjetsa JDR Stars 2-0 ndi zigoli za katswiri waku Namibia, Bethuel Muzeu kuti timuyi isunthe kwambiri mu ligiyi. Mmasewero, katswiri waku Malawi, Raffick Namwera, ndiyemwe anali mtsogoleri wa osewera a Leopards.
Zateremu, timuyi ili ndi mapointsi 7 pa masewero asanu ndi amodzi (6) ndipo yafika pa nambala khumi pa matimu 16.
Mponda anatenga ntchitoyi sabata yatha pomwe mphunzitsi watimuyi anamuchotsa ndipo tsopano waipezetsa timuyi zipambano ziwiri mu ligiyi.
Nice job
CIVO YALEMBERA SULOM PA MLANDU WA MOYALE
Timu ya Civo United yalembera kalata bungwe la Super League of Malawi kuti lilowepo ndikuunikira nkhani yoti timu ya Moyale Barracks inalowetsa osewera yemwe anali ndi makalata achikasu atatu ndipo samayenera kusewera.
Timuyi yachita izi atatha masewero omwe anagonja 1-0 ndi chigoli cha Charles Nkhoma zomwe zawapangitsa kuti akhalebe ku chigwa cha matimu otuluka.
Mmasewerowa, Clifford Chimulambe wa Moyale Barracks, anali mu gulu la osewera omwe analowa mmasewerowa koma samayenera ndipo Moyale inamutulutsa patangotha mphindi ziwiri zomwe zinapangitsa Civo kufufuza.
Zateremu, Moyale ili pa chiopsezo cholandidwa ma pointsi onse atatu omwe atha kupereka ku Civo kamba ka mlanduwu.
Good work #maule today
👉👉
KULIBE MANTHA KU SCORCHERS
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati palibepo mantha aliwonse omwe akuoneka mu timu yake pomwe tsopano amaliza zokonzekera zonse kuti akumane ndi South Africa lachitatu mu mpikisano wa COSAFA.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati zokonzekera zonse zatha bwino ndipo akukhulupilira kuti achita bwino mmasewerowa.
"Tinayenda bwino kuchoka kumudzi kufika kuno tinapanga zokonzekera dzulo, leronso tapanga zina kuziongola ndi kukonza mwina motsalira. Palibe mantha aliwonse Poti tikukumana ndi eni khomo ndipo kupambana mmasewerowa kutithandiza kuchulukitsa mwayi ofika ndime zina." Anatero Fazili.
Masewerowa ayamba nthawi ya 15:30hrs masana ndipo akhale oyamba mu gulu lawo.
"RED LIONS SI TIMU YOTI YATULUKA KAPENA YOPHWEKA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati wawauza osewera ake kuti asayiphweketse Red Lions ponena kuti akhale masewero ovuta kukumana nayo.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo omwe ali pa bwalo la Karonga lachitatu ndipo wati timu yawo ikufunikira mapointsi onse atatu kuti imalize pabwino mu ligiyi.
"Red Lions si timu yoti yatuluka kapena kuti mwina ikuvutika nde zikakhala zophweka ayi. Tawauza osewera kufunikira kopeza chipambano mmasewerowa ndipo lachitatu tikuyembekeza kuchita bwino." Anatero Kajawa.
Iye wati Nanson Mbewe yekha ndi yemwe sapezeka kamba koti ali ndi makadi achikasu atatu. Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi 33 pa masewero 23 mu ligi.
"NGATI BANGWE TIKUNGOFUNA CHIPAMBANO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati sizikuwakhudza kuti timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili ndi mkwiyo ogonja mu CAF Champions league koma iwo akufuna mapointsi atatu basi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe matimuwa akukumana pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo wati akudziwa kuti Bullets ndi yaikulu komanso osewera apangongole sasewera koma ali ndi anyamata ena aluso.
"Tikudziwa kuti Bullets ndi timu yaikulu komanso ndi mmene zachitikira kunja kuja afuna azitolere msanga koma ndife okonzeka. Ali ndi mphunzitsi wabwino komanso osewera apamwamba koma ifenso tili ndi osewera aluso, sitikuopa chifukwa tonse tili mu ligi." Anatero Mkandawire.
Atakumana mu gawo loyamba, Bullets inapambana 2-0. Bangwe All Stars ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri pomwe yatolera mapointsi 31 pa masewero 22.
Next game for ntaja united
"CIVO SIKUTULUKA MU LIGI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake sikutuluka mu ligi ndipo masewero asanu ndi awiri omwe atsala nawo ndi okwana kuti atsale mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonja 1-0 ndi timu ya Silver Strikers loweruka kuti akanike kutuluka mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi. Iye wati zikuvuta koma Civo singatuluke mu ligiyi.
"Tinayenera kuti tizipambana masewero chifukwa zinthu sizili bwino komabe tatsala ndi masewero 7, sitinadine batani la ngozi mwina kungotsimikiza, Civo situluka." Anatero Chidati.
Padakali pano, timuyi ili ndi mapointsi 25 pa masewero 23 omwe asewera mu ligiyi ndipo ali pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) mu ligiyi.
"I'M TIRED NOW, ITS BECOMING BORING' - HARRISON ON OFFICIATION
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says he is now tired with poor decisions by officiating panel as they keep on hurting the team in every game.
The Englishman said this in response to his protests during the match when Mwai Msungama denied the Nomads a clear penalty and what it looked like a clear goal as they beat Extreme FC 3-0 in the league. He said it's now becoming boring.
"I'm now tired, I'm tired every week we get handled every game we got cheated in their decisions against us when a penalty follows or against our goal, like Gaddie's, it was clear. Come on guys its now becoming boring." Said Harrison.
The Nomads faced an error from Godfrey Nkhakananga that cost them to abandon a game against Silver while against Blue Eagles, a dubious penalty was given against them.
SANUDI NDI OYAMBA KUTHANDIZA ZIGOLI KHUMI CHAKA CHINO
Katswiri wotseka kumbuyo wa Mighty Mukuru Wanderers, Stanley Sanudi, wakhala oyamba mu ligi ya 2023 kuthandiza zigoli khumi mu ligiyi kutsatira kuthandiza zigoli ziwiri mmasewero omwe Wanderers yapha Extreme FC 3-0.
Sanudi anamenya ma kona angapo koma awiri anafikira pa mutu pamzake otsekanso kumbuyo, Lawrence Chaziya yemwe anasumbira mu ukonde kuti katswiriyu akweze nambala yake yothandizira zigoli.
Katswiriyu tsopano wathandizira zigoli 10 mu ligiyi ndipo wapambuyo pake ndi Patrick Mwaungulu wa FCB Nyasa Big Bullets yemwe wathandizira zigoli zisanu ndi zitatu (8).
Osewera monga Wisdom Mpinganjira, Chimwemwe Idana komanso Stain Davie athandizira zigoli zokwana zisanu ndi ziwiri (7).
"SITINATULUKIRETU, MWENDO WINA ULI MKATI" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati zinthu zikuoneka kuti zikuvutabe koma timu yake sinatulukiretu mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 3-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu lamulungu ndipo wati awauza anyamata ake kuti asataye mtima.
"Tingowauza kuti alimbikirebe pa masewero omwe atsalawa, masewero 6 ndi ambiri amenewa, mwina omwe ali pamtunda pathu tikusiyana mapointsi 6 nde kupambana atatu kapena anayi zitha kusintha zinthu. Mwina mwendo wina watuluka wina ukadali mkati nde tiyikabe mtima mwina chozizwa ndi kubwera." Anatero Kafoteka.
Extreme itati yapambana masewero awo onse omwe yatsala nawo, itha kufika pa mapointsi 32 koma apa ilinawo 14 pa masewero 24 omwe yasewera.
"TIWALIMBIKITSABE ANYAMATA KUTI TITHERE PABWINO" - MPINGANJIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Albert Mpinganjira, wati awalimbikitsa anyamata atimu yake kuti asafooke kuti athere pa nambala yabwino mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Extreme FC 3-0 mu ligi ndipo wati anyamata ake anaphonya kwambiri komabe awalimbikitsa kuti azipeza zigoli.
"Mmene ligi ilili zigoli zimafunikanso nde koma taphonya kwambiri, mwina tikanapambana 8 olo 7 komabe tiwalimbikitsa kuti azitha kugoletsa zambiri. Tiwalimbikitsa kuti achilimikebe kuti tione kuti tithera pati." Anatero Mpinganjira.
Timu ya Wanderers tsopano ili pa nambala yoyamba ndi mapointsi 46 pamasewero 23 omwe yasewera.
TABITHA WAYAMBA NDI KUGONJA
Katswiri wa Scorchers, Tabitha Chawinga, wayamba movuta kwambiri ku timu ya PSG pomwe timuyi yagonja mmasewero ake oyamba omwe iyeyu wasewera.
Chawinga anayamba masewero omwe amakumana ndi akatswiri a mdziko la France, Olympic Lyonnaise ndipo anavala malaya a nambala 22 mmasewerowa.
Lyon inapeza chigoli chawo mu chigawo choyamba ndipo inakwanitsa kuzitchinjiriza mpakana kumapeto a masewerowa kuti ithere 1-0.
Uyu ndi chiyambi cha moyo wina kwa Chawinga kutsatira kupita kutimuyi pangongole kuchokera ku timu ya Wuhan Jiangda yaku China.
MBAVA ZAKUMPIRA ZIONA MAVUTO
Zachinyengo ku masewero a mdziko muno zikuyembekezeka kutha pomwe bungwe la Football Association of Malawi yapanga mgwirizano ndi bungwe lothana ndi Katangale la Anti Corruption Bureau (ACB) mammawa a lolemba.
Mtsogoleri wa FAM, Walter Nyamilandu Manda, wati ndi mgwirizanowu zoipa zomwe zimachitika kumpira tsopano zichepa pomwe zambiri sizimabwera poyera.
Mkulu wa ACB, Martha Chizuma, wachenjeza kuti samvera chisoni wina aliyense koma olakwitsayo anjatidwa kuti alandire chilango. Iye wati amakanika kulowerera ku mpira kamba koti amasowa mpata ngati umenewu.
Komiti ya anthu khumi ipangidwa pansi pa mgwirizanowu ndipo zina mwa zomwe azifufuza ndi mmene osewera amatengedwera ku Flames, osewera kusintha matimu, za oyimbira komanso ndalama zapachipata.
DE JONGH AKUBWERA LACHINAYI
Mphunzitsi wa timu ya Silver Strikers, Pieter De Jongh, afika mdziko muno lachinayi likudzali pomwe tsopano mapepala ake atheka kuti apitilize ntchito yake.
Mneneri watimuyi, Willard Chakanika, watsimikiza kuti timuyi yapangitsa chitupa cha zaka ziwiri tsopano pomwe Silver yalipira K2 million imene inkafunikira kugwirira ntchitoyi.
Mphunzitsiyu ali mdziko la Kenya komwe kuli banja lake komwe anapita pa 22 September 2023 kamba koti chitupa chake chakale chinatha mphamvu.
Mu nthawi imene iye kunalibeko, Silver yakwanitsa kugonjetsa Mighty Mukuru Wanderers komanso Civo United mu Airtel Top 8 ndi Supa ligi iliyonse.
Extilime chilimikan
Fixtures