MANOMA AMVEDWA PA MLANDU WAWO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers tsopano yatula nkhawa zawo pomwe loweruka inakumana ndi akuluakulu a bungwe la Football Association of Malawi posagwirizana ndi chigamulo chomwe bungweli linapereka ku timuyi.
Manoma anatsogozedwa ndi a Kalekeni Kaphale ndipo anaperekezedwa ndi David Kanyenda, Chancy Gondwe, Limbani Magomero, Roosevelt Mpinganjira, Chimwemwe Kaonga, mphunzitsi Mark Harrison komanso Stanley Sanudi.
Kaphale wati FAM inalakwitsa posaitana Wanderers popanga zinthu zawo zomwe ndi zotsutsana ndi FIFA, malamulo a Airtel Top 8 sangapose malamulo a FIFA oti chiganizo cha oyimbira ndi chotsiriza komanso kuti manambala a mipando anachoka bwanji pa 70 kufika 239.
Iye wati bungweli lichotse chilango chomwe inapereka kwa Wanderers. Williams Banda, Raphael Humba, Alfred Gunda ndi Gomegzani Zakazaka ndi omwe amayankhapo ku FAM ndipo Allison M'bang'ombe ndi yemwe amatsogolera mkumanowu pomwe okumva milandu, Khumbo Soko ndi Ted Roka anali pomponso.
Chiga
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores