"SITIKUYIMIKA MANJA MMWAMBA MONGA RED LIONS" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu ya Red Lions iyesabe mmasewero awo omwe atsala kuti imenyere nkhondo yosatuluka mu ligi pomwe wati iwo sanatuluke.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Balaka ndi Kamuzu Barracks ndipo wati kuchinyitsa mwachangu ndi komwe kunawapweteketsa koma ayesetsa mmasewero omwe yatsala nawo.
"Tivomereze kuti tatayadi mapointsi, sitinasewere monga mwa plan yathu mwina zigoli tinachinyitsa koyambilira zinatibalalitsa tivomereze kuti taluza. Masewero akadalipo, sitikufooka mmasewero omwe atsalawo tiyesetsa kuti tiwine." Anatero Masapula.
Timu ya Red Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero okwana 25 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores