"OSEWERA SANALI BWINO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake sinali bwino mchigawo choyamba zomwe zapangitsa kuti agonje 3-2 ndi timu ya Extreme.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Nankhaka ndipo wati akakonzanso mavuto awo kuti lachitatu akamakumana ndi Kamuzu Barracks adzakonze zonse.
"Sitinasewere bwino mchigawo choyamba pomwe anzathuwa anatichinya koma zimachitika kuti anthu osadzuka bwino mu mpira. Mchigawo chachiwiri titawayankhula zinthu zinasintha, tinasewera bwino mpaka tinapezako zigoli." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe yavutika kuti itolerere mapointsi bwinobwino mmasabata angapo pomwe ili pa nambala 9 ndi mapointsi 32 pa masewero 25.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores