"OSEWERA ATHU AWIRI APITA NAWO KU CHIPATALA" - SIMKONDA
Mtsogoleri wa osewera atimu ya Moyale Barracks, Gastin Simkonda, wati timu yawo sinyamuka lero kumapita ku Mzuzu kuti amakonzekere za masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati sangayende bus yawo ili yosweka.
Iye amayankhula izi kutsatira kuphwanyidwa kwa galimoto yomwe amayendera ndi anthu aku Dedza pomwe timuyi inalepherana 1-1 ndi Dedza Dynamos ndipo wati zimenezi si zampira pomwe Chifundo Damba ndi Timothy Nyirenda onse avulazidwa.
"Timalimbikira zokonzekera kuti tizichita bwino komanso pa bwalo la zamasewero timalimbikiranso koma oyimbira akumatisokoneza lero awapatsa penate yabodzanso chabwino tayivomera kenako akutigenda ndi kutiphwanyira bus yathu mpaka anzathu awiri athamanga nawo ku chipatala." Anatero Simkonda.
Iye wati ndi zovuta kuyenda kamba ka mphepo ndi zinthu zina ndipo wati si zampira. Mkulirano unabuka pomwe osewera a Moyale amafuna kumugwira nthupi oyimbira kamba ka penate yomwe anaipatsa Dedza Dyna
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores