"SI IFE OKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu yake siyokhutira ndi kufanana mphamvu ndi Silver Strikers pomwe amafunikira chipambano ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 pa Chitowe ndipo wati akonza mavuto awo pomwe akukakunana ndi timu ya Karonga pa bwalo lamulungu likudzali.
"Sife okhutira ndi zotsatirazi, timayenera kupambana chifukwa ndi mmene ligi yavutiramu mapointsi atatu ndi ofunikira koma tatenga imodzi basi tingovomereza." Anatero Mwansa.
Iye wati masewero awo ndi Karonga akhala ovuta kamba koti akakumananso ndi timu yabwino koma ayesetsa kukonza mavuto awo ngati kuphonya Kwambiri kuti akapambane masewerowa.
Timu ya MAFCO ili pa nambala 9 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 32 pa masewero 25 ndipo yatsala ndi masewero asanu kuti amalize mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores