"TINAWAUZA ANYAMATA KUTI AKAFERE MU BWALO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati ndi wokondwa ndi mmene timu yake inasewera ndi Moyale Barracks pomwe wati masewerowa amaonetsa tsogolo la timuyi mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Moyale Barracks 3-0 pa bwalo la Kamuzu koma wati akufunikirabe kupambana mmasewero omwe atsala nawo kuti athere pabwino.
"Anali masewero ofunikira kwambiri potengera kuti amationetsa tsogolo lokhala mu ligi nde ndithokoze anyamata analimbikira kuchinya Moyale 3-0 si zophweka koma zatengera kulimbikira kwawo. Apapa ntchito ikadalipo chifukwa ligiyi yavuta kwambiri." Anatero Nyambose.
Iye anatinso kutsogola masewero omwe asewera kulibe ntchito koma kumapambana poti Fodya umanena wapamphuno. Tigers ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi 31 pa masewero 26.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores