"BWALO SILABWINO KOMANSO PANALI MPHEPO YAMBIRI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets wati kuipa kwa bwalo la Rumphi komanso mphepo zimapangitsa kuti timu yake ikanike kusewera bwino pomwe yalepherana 1-1 ndi Ekwendeni Hammers.
Iye amayankhula atatha masewerowa ndipo wati anali masewero ovuta kutengera kuti timu ya Ekwendeni Hammers nayo inachilimika mmasewerowa.
"Choyamba tithokoze Mulungu kuti tapeza zotsatira zimenezi, sanali masewero ophweka ndipo anyamata athu anapeza mipata yoti akanatha kupeza zigoli koma aphonya. Inde bwalo silili bwino komanso mphepo komabe tinawauza anyamata kuti asewerebe." Anatero Munthali.
Timu ya Bullets ikadali pa nambala yachiwiri mu ligiyi pomwe ali ndi mapointsi okwana 44 pa masewero 21 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores