"OYIMBIRA NDI YEMWE WATIPWETEKA" - SOSTEN
Wapampando wa timu ya FOMO FC, Hadweck Sosten, wati timu yake yagonja chifukwa choti oyimbira, Mayamiko Kanjere, amakondera timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Kanjere akumudziwa kale kuti sayimbira bwino.
"Anali masewero abwino, tamenya bwino kwambiri muone timasunga mpira kwambiri kuposa iwowa timawamenya koma oyimbira ziganizo zake sizinali bwino. Anawapatsa penate yabodza pomwe iwo akagwira samayimba nde iyeyu watipweteka." Anatero Sosten.
Iye watinso timuyi ilowa mu Supa ligi ya chaka cha mawa. Kutsatira kugonjaku, timu ya FOMO ikadali pa nambala yachiwiri mu gulu B ndi mapointsi 33 pa masewero 18.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores