MALAWI YAMALIZA BWINO MU GULU A
Timu ya Scorchers yapanga mbiri yapaderadera pomwe yapambana masewero awo onse amugulu pomwe apambana 3-1 kugonjetsa timu ya Madagascar masana a lachiwiri ku South Africa.
Vanessa Chikupira anatsogoza Malawi pa mphindi 22 asanabwere Leticia Chinyamula pa mphindi 24 koma Madagascar inabwenza chimodzi pa penate ndipo Asimenye Simwaka anagoletsa chigoli chapamwamba kuti timuyi itsogole 3-1 pa mphindi 38.
Mmasewerowa, osewera akuluakulu ngati Temwa Chawinga, Chimwemwe Madise ndi Madyina Ngulube sanalowe. Mmasewero ena, timu ya South Africa yagonjetsa timu ya Eswatini 3-0 kuti imalize pachiwiri.
Malawi yafika mu ndime ya matimu anayi ndipo Zambia ndi Mozambique afikanso mu ndimeyi pomwe amu gulu C sanadziwike.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores