"OSEWERA ANAKOMEDWA NDI SAPOTI YA PANJA" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati osewera atimu yake anakomedwa ndi ochemerera nthawi yomwe anapeza chigoli chawo zomwe zinachititsa kuti atayilire.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati mipata yomwe anaipeza akanagoletsa zikanatha kuwachitira ubwino.
"Anali masewero abwino kwambiri tinapeza mipata yoti tikanagoletsa tikanatha kupambana komabe sizinatheke komabe zotsatira izizi zitilimbikitsa. Atapeza chigoli anakomedwa ndi phokoso la ochemerera nde anatayilira." Anatero Mauluka.
Iye wati timu yake sikungoyang'ana zotsala mu ligi koma kuti ithere mu matimu 8 oyamba mu ligi. Iwo ali pa nambala 13 ndi mapointsi 30 pa masewero 26.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores