"TIKUFUNA TIKWERE MU LIGI" - CHIRWA.
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati masewero atimuyi ndi Red Lions anali ofunikira kwambiri pomwe akuyang'ana kuti athere pa nambala yabwino mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Red Lions 2-0 pa bwalo la Balaka ndipo wauza ochemerera atimuyi kuti iwo agwira ntchito yotamandika.
"Anali masewero ofunikira kwambiri kuti tikwere mu ligi nde 2-0 kupambana ndine okondwa kwambiri. Masapota akhalebe nafe, ife tiyesetsa kuti tigwire ntchito ndipo timaliza pa bwino ndithu." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks tsopano yasuzumira ku matimu anayi oyamba mu ligiyi pomwe ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 39 pa masewero 25 omwe yasewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores