"ULENDO UNO WOKHA MULUNGU ALINAFE TITENGA COSAFA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati nsi wokondwa kamba koti timu yawo yafika mu ndime yotsiriza ya chikho cha COSAFA ndipo wati ulendo uno ayesetsa kuti agonjetse Zambia.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Mozambique 2-1 mu ndime ya matimu anayi kuti afike mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu. Iye wati sakuyiopa Zambia ndipo lamulungu akungofuna chikho basi.
"Zambia ndi masewero ovutanso koma Pali zifukwa zimene amatigonjetsera mmbuyomu koma panopa mbiri singagwirenso apapa Zambia ikagwira magobo kuti itigonjetse koma Mulungu ali mbali yathu titenga chinthuchi." Anatero Fazili.
Malawi inatsalira ndi Mozambique kudzera mwa chigoli cha Lonica Tsanwane koma Temwa Chawinga anapeza zigoli ziwiri kuti ipambane. Masewero ndi Zambia achitika lamulungu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores