"LERO TIMASEWERA NDI ANTHU 14" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati ngati oyimbira aziyimbira ngati mmene anachitira mmene amakumana ndi Karonga United siziziyenda bwino ndipo wati wawapweteka.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Karonga United pa bwalo la Karonga ndipo wati vuto lomwe lakula ndi loti pali chimene chikusintha akadandaula za oyimbira nde angozitaya.
"Kunena zoona atolankhani mumaona oyimbira athuwa ngati zizitero nde siziziyenda bwino. ziganizo zonse zinali zokondera enawa mwina titha kuti tasewera ndi anthu 14 komabe poti palibe chimene chikumachitika basi tibwerera kwathu." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe yapeza mapointsi 32 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores