"OSEWERA ACHISODZERA APATSIDWA MPATA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati osewera achisodzera omwe anapita ndi timuyi apeza mpata osewera pomwe timuyi ikumane ndi Madagascar mu masewero omaliza a gulu A.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake sikudelera komanso ikufunitsitsa kuti imalize ndi zipambano zitatu mu gulu mwawo.
Iye wati mmasewerowa apereka mpata kwa osewera achisodzera kuti aziphunzirako kwa akuluakulu ndikuti timuyi ikhalebe ya mphamvu mpaka kale.
"Tikuyembekeza masewero abwino, Madagascar ndi timu yabwino ndipo itha kutidzidzimutsa komabe tikufuna kupambana masewerowa. Osewera achisodzera asewera mawa kuti achotseko mantha." Anatero Fazili.
Timu ya Scorchers inafika kale mu ndime ya matimu anayi pomwe inagonjetsa South Africa ndi Eswatini mu gululi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores