Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Hello guys to be honest mpira waku malawi ....ndiosangalatsa and please amene mumaona za ma sapota plz make sure that ma sapota anu mukuwalangiza bwinobwino so that mpira usabweretse kuonongeka kwa katundu wa boma
Who wins in penalty mafco and kb
No post match penalties were played. Mafco won through away goal rule.
EXTREME YATULUKA MU LIGI
Timu ya Extreme FC yakhala yoyamba kutuluka mu ligi ya chaka chino kutsatira kugonja 2-1 ndi timu ya Red Lions pa bwalo la Balaka masana a loweruka.
Deus Nkutu ndi Mike Kaziputa anagoletsa zigoli za Lions pomwe Beston Jimu anamwetsako cha Extreme kuti Lions itsalebe ndi mwayi otsala mu ligi. Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Elvis Kafoteka, wati unali ulendo wovuta mu ligiyi.
"Wakhala ulendo wosasangalatsa kwambiri chifukwa masewero oti tiziwina timaluza koma ovutawo timawina nde mwina tikanakhala kuti timakhazikika pa zochita anyamatawa bwenzi atatsala mu ligi." Anatero Kafoteka.
Timuyi ili pa nambala 16 ndi mapointsi 18 pa masewero 27 omwe yasewera ndipo yasewera mu ligiyi kwa chaka chimodzi tsopano ikubwereranso mu Chipiku Stores Central Region Football league.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"TIKHONZA KUTSALIRABE MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu yake tsopano ili ndi mwayi oti itha kutsala mu ligi pomwe tsopano akufunikira kuchita bwino mmasewero awo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Extreme FC 2-1 pa bwalo la Balaka ndipo wati mmene anyamata ake akuchitira, akupereka chilimbikitso kuti atsala mu ligi.
"Kukonzekera kwathu kunali kwa pamwamba chifukwa timadziwa kuti masewero alero ndi apampeni koma tithokoze kuti tawina. Mwayi ulipo wochuluka, anyamata akuonetsa kuti ali tsopano bwino koma asamasuke kuti alibwino chifukwa zikhonza kuwasokonekera." Anatero Masapula.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi ndipo yatsala ndi masewero okwana atatu kuti imalize ligi ndipo ikufunikira mapointsi anayi kuti ichoke ku chigwa cha matimu otuluka ndipo ili ndi mapointsi 25.
"BULLETS INALI BWINO PA CHILICHONSE" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati kuchinyitsa changu mmasewero omwe amasewera ndi FCB Nyasa Big Bullets ndi kumene kwawapweteketsa pomwe wati ndi zovuta kuti kuchokera kumbuyo ndi matimu ngati amenewa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Bullets inali bwino pa chilichonse angakhale kuti anyamata ake anayesetsa.
"Anzathuwa anachenjera chifukwa anagoletsa mwachangu nde ndi zovuta kwa timu ya masapota ochuluka chonchi kuti ungabwenze poti uyu ndi osewera wachi 12 nde awa ndi ana akadaphunzira anayesetsabe komabe Bullets inali bwino pa chilichonse." Anatero Mtetemera.
Masewero otsatira ndi okumana ndi timu ya Civo United lachitatu ndipo timuyi ikadali pachinayi ndi mapointsi okwana 43 pa masewero 25 omwe yasewera.
"SITIKUYANKHULIRATU ZA CHIKHO KOMA TIPANGE ZA MASEWERO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake tsopano sikuyang'ana zoti ikasewera masewero angapo iyandikira chikho koma iwo akupanga za masewero aliwonse pa okha.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa United 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake inali bwino pokwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri.
"Sitinganene kuti tavutika, tagoletsa zigoli ziwiri koma kungoti anzathuwa anabweranso ndi mtima woti akugonjetse paja anatichinya 1 koma leroli anyamata analimbikira tapambana 2. Sitikuyang'ana zoti tatsala ndi masewero motani, zambiri tidzayankhula mmasewero otsiriza amu ligi." Anatero Munthali.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikutsogolera ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 50 pa masewero 23 omwe yasewera ndipo yatsala ndi masewero awiri kuti afanane ndi omwe yamenya Wanderers yomwe ili pachiwiri.
MAFCO YAFIKA MU NDIME YAMATIMU ANAYI MU AIRTEL TOP 8
Timu ya MAFCO yakhala yoyamba kuzigulira malo amu ndime ya matimu anayi amu chikho cha Airtel Top 8 kutsatira kulepherana 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks koma iwo apitilira kamba kogoletsa koyenda.
Dan Chimbalanga anamwetsa pa mphindi yoyamba yeniyeni koma Olson Kanjira anabwenza pa mphindi zinayi kuti masewero athere 1-1 zomwe zinasangalatsa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti KB nayo inasewera bwino kwambiri koma tiyamike anyamata poti anachita zimene tinawauza zilibwino kuti tafika mu ndimeyi yomwe ndi yovuta kuti tikadutse koma chanzeru ndi choti tapitilira." Anatero Mwansa.
Timuyi tsopano idikilira matimu ena atatu omwe awatsatire mu ndimeyi ndipo imodzi idziwika lamulungu pomwe Blue Eagles ikulandira Moyale Barracks pa Nankhaka ndipo masewero ali 1-1.
"TIKUDABWA KUTI MPIRA WATHU UKUYENDA BWANJI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati wadabwa ndi uthenga woti timu yake yatuluka mu Airtel Top 8 chonsecho pa nkumano womwe unalipo masewero asanayambe anati akalepherana ifika ku mapenate.
Kalinda amayankhula izi atatha masewero omwe atuluka mu chikhochi angakhale kuti alepherana 1-1 ndi MAFCO ndipo wati chiganizo choti yochinya koyenda ipitilira chabwera kutangotsala mphindi zisanu.
"Ndikudabwa kuti akuti tatuluka malamulo azikhala mmene alili, ku mkumano masewero asanayambe anatikumbutsa kuti masewero kaya atha 1-1 kaya 0-0 afika ku mapenate koma kutatsala mphindi 5 ndi pomwe akuti zikatha chonchi MAFCO ipitilira." Anatero Kalinda.
Iye wati ngati kuli kukamang'ala pa nkhaniyi si mbali ya aphunzitsi a timuyi komatu akuluakulu a timuyi. Zateremu timuyi yatuluka mu chikhochi ndipo maso awo ayang'ana pa Castel Challenge Cup ndi TNM Supa ligi.
"WE NEED TO WIN TO PRESSURIZE BULLETS" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says he is not giving up on winning the league and that he will do that when it is mathematically impossible.
He said this on Saturday ahead of their match against Dedza Dynamos in Dedza and said a win will be important for it will keep on pressurizing FCB Nyasa Big Bullets who are topping the league.
"It looks like Bullets have probably pulled another three points today. So we need to try to get points so that we keep pressure on Bullets . It is important. We need to show a little bit of aggression in the field in our play. With and without the ball we need to put more pressure into teams." Said Harrison.
He further said he will try to win all the remaining five matches which will give pressure to Bullets and as Nomads, they will still fight. They are second with 47 points from 25 games.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
CHAWINGA WAGOLETSANSO KU PSG
Katswiri wa timu ya Scorchers, Tabitha Chawinga, akupitiliza kuchita bwino ku timu yake ya PSG pomwe loweruka wagoletsanso chigoli chake chachitatu ndi timuyi pomwe yagonjetsa Lille 4-0.
Chawinga anamwetsa chigoli chachiwiri cha timuyi mmasewerowa pomwe Katoto anali ataitsogoza kale ndipo Baltimore anamwetsa chigoli chachitatu kuti ikhale 3-0 popumulira.
Mchigawo chachiwiri, Vangsgaard anakhoma nsomali omaliza kuti timuyi ipambane mmasewerowa 4-0. Chawinga tsopano ali ndi zigoli zitatu zamuligiyi mmasewero anayi ndipo chimodzi ndi chamu UEFA champions league.
TNM super league standings
"THERE'S NO LONGER A SMALL TEAM IN THE LEAGUE" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says he expects a tough match against Chitipa United on Saturday afternoon and that a poor approach to the game might cost them.
The Zimbabwean said this ahead of the match involving the two teams at the Kamuzu Stadium as the People's team seek for a revenge following a 1-0 loss in the first round. He said the league has no small team and in every game, a good approach is vital for them to win.
"Football is all about how you approach it, remember we've got two legs and they have two legs, in a match you are supposed to field 11 players and us will be fielding 11 players then mentally, if we take ourselves to say we are Bullets, end result we lose." Said Pasuwa.
He further said he talked about the so called small teams when the league was kicking off and that there's a proof of not having small teams in the league currently. Bullets are top with 47 points from 22 games.
nyasa bg bules
All games tnm games remaining forFCB nyasa bullets
Manchester United legend and England World Cup winner Sir Bobby Charlton has died at the age of 86.
RIP Champion 🙏
Dedza Dynamos looking from far from an eye of a common person, seems to be a great team. Guess their performance will keep on improving.
https://shorturl.at/joV07
PSG YA TABITHA YATOLA JOCKER
Timu ya PSG ya amayi yomwe kuli wosewera wa Scorchers, Tabitha Chawinga, ikuyembekezeka kukhala ndi ntchito yovuta kwambiri pomwe yaikidwa mu gulu lovuta kwambiri mu UEFA Women's Champions League lero.
Timuyi yaikidwa mu gulu C la mpikisanowu pamodzi ndi matimu a Bayern Munich yaku Germany, Roma yomwe ndi akatswiri aku Italy komanso timu ya Ajax yaku Netherlands.
Mayerewa anachitira mammawa a lachisanu ndipo timu ya PSG inazigulira malo ake mu ndime yamaguluyi itakwapula Manchester United 4-2 ndipo Chawinga anagoletsa ndi kuthandiza chigoli chimodzi mwa zinayizi.
Chawinga wakhala wosewera oyamba wa mpira wamiyendo wa amayi ku Malawi kusewera mu UEFA champions League, kugoletsa chigoli mu mpikisanowu komanso kusewera mu ndime yamagulu a chikhochi.
#KasongaJr
MAFUTA BWITIBWITI KU NTOPWA
Timu ya mpira wamiyendo koma ya atsikana ya Ntopwa Super Queens, yaponda mwala pomwe yapeza thandizo kuchokera ku kampani yopanga mafuta ya Capital Oil Refining pansi pa Kukoma Cooking Oil brand.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lachisanu pomwe yati tsopano dzina la timuyi lisintha ndipo izitchedwa Kukoma Ntopwa Super Queens kamba ka thandizoli.
Ndondomeko za mgwirizano wawo ziululika sabata ya mawa pomwe kukhale mwambo waukulu osainirana ma pepala pa mgwirizanowu.
Timuyi inachita mbiri yokhala timu yoyamba yaku Malawi kutenga nawo mbali mu chikho cha COSAFA CAF Women's Champions League womwe unachitikira ku South Africa ndipo mu timu ya Scorchers anatumizamo osewera atatu.
FAM IKAMBIRANA ZA MPHUNZITSI WA FLAMES LERO
Komiti yaikulu ya bungwe la Football Association of Malawi ikumana mtsiku la lero ku Mpira house ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre kuti akambirane yemwe atenge ntchito ya mphunzitsi watimu ya Flames.
Izi zikudza pomwe timuyi ilibe mphunzitsi kamba koti mgwirizano wa Patrick Mabedi unatha mu September pomwe anatenga mmanja mwa Mario Marinica mu mwezi wa April.
Ndipo bungweli likuunikira dzina la Mabedi pamodzi ndi aphunzitsi 50 amdziko muno ndi akunja omwe analemberanso pa ntchitoyi kuti alowe mmalo mwa Marinica.
Timuyi ikhale ndi masewero mwezi wa mawa amu gulu lopitira ku mpikisano wa 2026 FIFA World Cup pomwe adzakumane ndi Liberia koyenda komanso Tunisia pakhomo.
"TABWERA KU BLANTYRE KUDZATENGA 3 POINTSI BASI" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake ya Silver Strikers yapita ku Blantyre ndi cholinga chimodzi chokha chomwe ndi kudzatenga mapointsi atatu pa mwamba pa timu ya Mighty Wakawaka Tigers.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu likudzali ndipo wati akudziwa kufunikira kopambana masewerowa kamba koti ligi tsopano ikufunikira kumatolera mapointsi.
"Zokonzekera zathu zayenda bwino, osewera ambiri omwe anali ovulala abwino, tikudziwa Tigers si, timalemekeze matimu omwe tikumenya nayo koma pomwe yafikira ligi yavuta kwambiri komabe tikupita ku Blantyre kuti tikatenge 3 pointsi." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver ili pa nambala yachitatu mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 43 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi ndipo akusiyana mapointsi anayi ndi FCB Nyasa Big Bullets yomwe ili pamwamba.
"IT SEEMS PLAYING CHAMPIONS LEAGUE IS A CRIME NOW" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, has accused associations that release fixtures of different tournaments for not being cooperative with his team as he said they are being punished for playing the CAF Champions League.
Pasuwa said this because of congestion of fixtures in different tournaments in the country and said his players as humans need to be given time to rest.
"It's not normal for a player to do what we are doing now, I think I see now it seems it's a crime playing Champions League now. I think the gulus and bosses don't consider the team that plays in the Champions League while making their fixtures hence we are given these fixtures nearly two to three days to play games but remember these are human beings they need to recover." Said Pasuwa.
The team is coming from the North via Central region where they have played four games in a space of 10 days, one in FDH Bank Cup, one in Airtel Top 8 with t
Kumbukanisingini5@gmail.com
UYU NDI PLEYA YEMWE WAGWEDEZA MALAWI YONSE: FRANCISCO MADINGA
yamikan chessta
CHAWINGA SHINES AS PSG QUALIFY FOR UCL
Scorchers captain, Tabitha Chawinga, produced a remarkable performance for her side, PSG, to help them qualify for the UEFA Champions League group stages for 2023/24 Season after knocking out Manchester United 4-2 on aggregate on Wednesday.
Chawinga scored a lone goal for her side in England as the two sides played a 1-1 draw and on Wednesday night, she made a brilliant solo run from the midfield but the goalkeeper denied her with a save and Martens guided the ball into the net on rebound on 17th minute.
United levelled on 47th minute through Naalson but the goal was short-lived as Chawinga made a brilliant run down the left to set Martens to restore the lead a minute later before Bartimore adding third from a very tight angle on 57th minute.
The Malawian lasted for 85 minutes as Katoto replaced her with United piling more pressure but a late disallowed goal and hitting the post could not save them from leaving the tournament early.
Meanwhil
How games bullets left to play
PLEYA YEMWE WAGWEDEZA MALAWI YONSE: FRANCISCO MADINGA
FCB NYASA BIG BULLETS WILL WIN THIS CUP
All the best Maule!
"PENANSO OYIMBIRAWA AMATHANDIZA ANZATHUWA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati wavomereza kugonja poti timu yake inapereketsa zigoli zophweka kwambiri koma wati oyimbira anaithandizakonso Bangwe All Stars.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 pa bwalo la Mpira ndipo wati ziganizo zina zimasemphana ndi mmene zimafunikira komabe mavuto awo akonza.
"Inde chabwino tagonja koma pena tizinena chilungamo oyimbirawa ah pena ziganizo zawo zinali zokomera anzathuwa, ma offside awo samayimba komanso ma free kick omwe amawapeza anali abodza koma tavomereza, ndi Wanderers sitizabwereza zolakwa zathu." Anatero Chirwa.
Timuyi tsopano yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi 35 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
"TIKUFUNA TSOPANO NAMBALA YACHISANU" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake ili ndi osewera achisodzera omwe akawauza zinthu amapanga ndipo wati akuyang'ana kuti amalize pabwino mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Dedza Dynamos 3-0 pa bwalo la Mpira lachitatu ndipo wati tsopano mmene apulumuka mu ligi, akuyang'ana zopambana masewero otsala kuti athere pa nambala yachisanu.
"Chipambano chokomadi anyamata anasewera bwino kwambiri, ndi anyamata aluso kwambiri oti ukawauza zinthu amapanga tawonani lero mpira wokongola ndipo tiwalimbikitsabe kuti mwina tifike nambala 5 kapenanso kumtunda." Anatero Mkandawire.
Kutsatira chipambanochi, Bangwe yagwetsa Dedza pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi 35 pa masewero 26 omwe yasewera.
Photo credit: Dedza media #KasongaJr
PHIRI JR AKUYESA MWAYI KU SWALLOWS
Katswiri wa Flames, Gerald Phiri Jr, akuyesedwa ndi aphunzitsi atimu ya Moroka Swallows ku South Africa ndipo ngati achite bwino ayamba kutumikira timuyi.
Phiri anapita mdzikomo kutsatira kuthetsa mgwirizano wake ndi timu ya Al-Hilal Omdurman yaku Sudan kamba ka nkhondo yomwe imachitika mdzikomo ndipo tsopano alibe timu.
Iye anachoka ku South Africa mgwirizano wake utatha ndi Baroka FC ndipo anapita ku Sudan komwe anasewera zaka ziwiri.
Ngati atasaine mgwirizano ndi Swallows, iye akhala osewera wachiwiri waku Malawi kusewera mu DSTV Premiership pomwe Gabadinho Mhango ndi yekha ali mu ligiyi.
WANDERERS TSOPANO IYANKHA PA MILANDU ITATU
Bungwe la Football Association of Malawi tsopano yaika milandu itatu yomwe timu ya Mighty Mukuru Wanderers iyankhepo pomwe inaononga mipando ya pa bwalo la Bingu komanso kukana kumaliza masewero omwe ankasewera ndi Silver Strikers.
Izi zadza pomwe zilango zomwe timuyi inapatsidwa zachotsedwa ndi cholinga choti akaimve kaye mbali yake asanawapatse chilango pa milandu.
FAM yati Wanderers ili ndi mlandu wosiya masewero kuti asathe zomwe ndi zosemphana ndi malamulo a Airtel Top 8, kuyambitsa ziwawa komanso kuphwanya mipando ya bwalo ndipo zonsezi zabala mlandu wachitatu wonyazitsa dzina la Airtel, FAM komanso mpira wamiyendo.
Padakali pano, Wanderers ikhala ndi tsiku limene ikakumane ndi komiti yokhazikitsa bata ku bungweli kuti akayankhepo pa mlanduwu.
Top goals
Fixtures
Bullets ndi A KATUNDU,akakhala pa top samasuntha pokhapokga akhale ndi ulendo opita kunja kwa dziko♨️♨️♨️♨️♨️♨️
Malawi yonse koma na uyu yekha ndikatundu
Kuipasa moto yekhaya ngatinso kuli mapuleya ena otinso ndimanvanawokukoma ndiye ndi chaziya komanso wisdom
Ndimakonda mighty mukulu wanderers ndiyomwe ndimasapota chimene ndimayikondela Ndichifukwa cha mapley awa gadie chira,wisdom mpinganjila,khristopher kumwembe,francisco madinga,stanly sanudi: Ndichifukwa ndimayikondela...
Mighty mukulu wanderers nditimu yomwe ili ndi ma pleya abwino malawi yonse.
SCORCHERS PLAYERS ARE MILLIONAIRES
Football Association of Malawi President, Dr Walter Nyamilandu Manda, has told people that Scorchers players will receive K1 million as a token for winning the COSAFA Women's Championship.
He said this at a gala dinner at Mount Soche Hotel in Blantyre which was organised to welcome the girls in the country. He said they have not gotten any money for winning the tournament but the money will be given to the girls.
He has further asked the corporate world to come and sponsor the Women's Football in Malawian as it has shown that it can reach higher heights faster than mens Football.
The team beat Zambia to clinch the trophy and finish the whole tournament unbeaten having scored 19 goals and conceded just 6 in 5 games.
Photo credit: ZBS
TNM
Mighty mukulu wanderers yomweyo Tomo kut buuuuuuuuu
ZILANGO KU SULOM ZAYAMBA POMWE EAGLES YALANDIRA
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu mdziko muno ya Super League of Malawi lapereka chilango kwa osewera anayi a timu ya Blue Eagles komanso wothandizira mphunzitsi watimuyi, Christopher Sibale, kamba koyambitsa zisokonezo pomwe ankasewera ndi Ekwendeni Hammers ku Mzuzu.
Mu kalata imene bungweli latulutsa lolemba lapereka chilango kwa kwa osewera atimuyi monga Sankhani Mkandawire, Tonic Viyuyi, Chakonda Majanga komanso Ranken Mwale kuti apereke K500,000 kamba kofuna kumenya oyimbira ndipo Mwale amupatsa chilango chosasewera masewero anayi.
Sibale naye alipira ndalama yokwana K500,000 kamba kochita nkhalidwe loyipa ndipo Blue Eagles ilipira ndalama zokwana K1.5 million kamba kokanika kuteteza anthu awo.
Ndalamayo ikuyenera kuperekedwa pasanathe masiku 14 ndipo pa mlanduwu, Blue Eagles inathamangitsa oyimbira kamba kosakhutira ndi kayimbilidwe mmasewero omwe anagonja 1-0 ndi Ekwendeni Hammers.
Maiki chizizombo
"PALIBE MWINI WAKE WA CHINTHU MU LIGIYI" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati iwo apitilizabe kumenya nkhondo kuti mwina china chake chichitika pomwe wati palibe mwini wake wa chinthu mu ligiyi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 ndi Blue Eagles ndipo wati ndi zopweteka poti achinyitsa kumapeto. Iye wati chimene ankafuna mu ligi anachipeza kwinaku ndi kungomenyera nkhondo basi.
"Ife chimene tinkafuna chinatheka komabe sizikutanthauza kuti tikhala chete, tipitilizabe kumenyera nkhondo poti palibe mwini wake wa chinthu mu ligiyi nde tiwalimbikitsabe osewerawa." Anafotokoza Mtetemera.
Timu ya Chitipa sinagonjebe pa bwaloli ngati akusewera pakhomo mu ligi ndipo yatsika kufika pa nambala yachinayi ndi mapointsi 43 pa masewero 24 mu ligiyi.
"TINANGOYIWERENGA MU ZOFOOKA ZAWO" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati kutenga point imodzi pamwamba pa Chitipa United ndi yofunikira kamba koti iwasuntha ndi mmene ligi yavutiramu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Karonga lolemba ndipo wati iwo anagwiritsa ntchito kuiona malo omwe akufooka kuti apeze zigoli zawo.
"Tinaona momwe akufooka nchifukwa chake tinapeza chigoli mwa changu kwambiri ndipo kumapeto tinawaona kuti atopa nde tinatenga ena ammbali kuti apite pakati kuti tichulukepo mpake tinapeza chigoli chobwenzera chija." Anatero Sibale.
Kutsatira kupeza point imeneyi, Eagles yasuntha kufika pa nambala 11 ndi mapointsi 31 pa masewero 26 omwe yasewera.
"MWAYI UKADALIPO OTSALA MU LIGI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsabe kumenyera nkhondo mmasewero omwe atsala nawo kuti mwina asatuluke mu ligi pomwe wati mwayi akadali nawo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Civo United 0-0 pa bwalo la Civo ndipo wati ndi wokhutira ndi zotsatirazi zomwe zithandize timu yawo.
"Poti tinali koyenda, point ndi yabwino ndipo ndasangalala nayo pomwe sitinagonje. Mwayi ukadalipo ndipo tikhala tikuyesabe kuti mwina tisatuluke koma mwayi ulipobe." Anatero Mkandawire.
Red Lions yatsala ndi masewero anayi ndipo akuyenera kupambana mmasewero onse kuti mwina angatsale mu ligiyi pomwe ali ndi mapointsi 22 pa masewero 26 pa nambala 15.
"SITIKUYANG'ANA ZA CHIKHO KOMA MASEWERO ALIWONSE" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wakana kuyikirapo mlomo pa nkhani yotenga chikho pomwe wati iwo amayang'ana za masewero omwe akusewera mtsiku limenelo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Mukuru Wanderers 1-0 pa bwalo la Bingu ndipo wati izi zilimbikitsa osewera kuti achite bwino mmasewero awo amtsogolo.
"Timanena kuti ngati osewera akudya bwino ndekuti azipambana masewero nde izi sizowakumbutsa mmasewero akubwerawa tilimbikira, ukachinya timu yaikulu umatayilira ukakumana ndi timu yaying'ono komabe zili ndi anyamatawa kuti achita bwanji." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver yafika pa nambala yachitatu pomwe yatolera mapointsi 43 pa masewero okwana 24 omwe asewera mu ligiyi.
"CIVO IKADALIPO MU LIGI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, walimbitsa mtima otsatira timuyi kuti satuluka mu ligi ndipo awonananso chaka cha mawa.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi timu ya Red Lions 0-0 ndipo wati timu yake ikusewera bwino koma mwina pa nambala yomwe ali ikumawapatsa phuma mpake akumaphonya.
"Kumbali ya lero timu yasewera bwino koma mwina nambala imene tiki ikumatipatsa phuma. Ndiwauze ochemerera kuti masewero tikanali nawo, atatu pakhomo awiri koyenda nde tikanali mu ligi." Anatero Chidati.
Timu ya Civo ili ndi mapointsi 25 pa masewero 25 omwe yaseweranso mu ligi ndipo ili pa nambala 14 mu ligiyi.
"WHY NOT TALKING ABOUT CHITIPA AND OTHER TEAMS?" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says coach for Mighty Mukuru Wanderers, Mark Harrison, talks about his team because he sees something in the People's team.
Pasuwa said this in an Interview with the team's media ahead of their match against Moyale Barracks on Tuesday and said Bullets do not talk about any team because their focus is on the pitch.
"Us is Bullets, we don't talk about other teams so if he [Harrison] is talking about us that's means he sees [fears] something in us. Why is he not talking about Chitipa United or other teams?" Questioned Pasuwa.
About their Moyale match, he said his players need to adjust themselves for the 'bad and windy' Rumphi Stadium so that they earn positive results. He also said Chawanangwa Gumbo will not be available due to an injury.
Bullets are second in the league having collected 44 points from 21 games, three points behind Wanderers which has played four games more.
"WE ARE RELYING ON BULLETS TO DROP POINTS" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says it will become hard for his team to win the TNM Super league this season after dropping 7 points in their past three games despite staying top.
Harrison said this after his team lost 1-0 to Silver Strikers at the Bingu National Stadium to move up to four games ahead of FCB Nyasa Big Bullets with only four points separating them. He says things could change if Bullets drop some points.
"Its becoming tight now, I mean we needed to win today but we've chopped it away, it will be tight now and we are relying on Bullets to drop points now you know [laughs]," said Harrison.
Chimwemwe Idana netted an 83rd minute strike for the Nomads to suffer their fourth loss this season and have 47 points from 25 games on top of the League.
Written by: Hastings Wadza Kasonga Jr
SCORCHERS YAFIKA NGATI MAFUMU
A Malawi ochuluka kwambiri anakhamukira mminsewu ya mzinda wa Blantyre kulandira timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi ya dziko lino kuchokera ku South Africa komwe apambana chikho cha COSAFA Women's Championship lero.
Timuyi yafika masana a lolemba kudzera pa bwalo la Chileka ndipo magalimoto ambiri, anthu odziwika ndi akuluakulu a boma anasonkhana pamodzi kufika pa bwaloli kuyilandira timuyi.
Iwo aonetsa chikhochi mu malo ngati Chileka, Kameza Roundabout, Chirimba, Che Mussa, Mbayani komanso ku msika waukulu wa Blantyre mpaka kukafika ku malo ogona a Sunbird Mount Soche ku Blantyre.
Iwo akhala ndi mwambo wa madyerero usiku wa lero pa malo ogonawa ngati njira yowalandira. Malawi inagonjetsa Zambia 2-1 kuti itenge chikhochi.