GHEDO LORENZO WAPAMBANA MPHOTO YOSEWERA BWINO PA MWEZI
Timu ya Chitipa United yasankha katswiri wawo womwetsa zigoli, Ghedo Lorenzo, kuti wapambana mphoto ya osewera bwino wa mwezi wa September atapeza mavoti ochuluka kuposa anzake awiri.
Timuyi yalengeza izi lachitatu madzulo kudzera pa tsamba lawo pomwe iye waposa Ramadhan Ntafu ndi Stain Patrick pa mphotoyi.
Iye anagoletsa Chigoli chokhacho pomwe timuyi inagonja 2-1 ndi Chitipa United komanso chimodzi pomwe anagonjetsa timu ya Bangwe All Stars 2-0 ku Blantyre.
Iye atenga ndalama zokwana K100,000 kamba kopambana mphotoyi. Osewera monga George Chikooka Rajab Nyirenda ndi Blessings Joseph apambanakonso mphotoyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores