"NGATI OSEWERA AKUFUNA NDALAMA AZIWINA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake yataya mapointsi pa masewero omwe akanatha kupambana ndipo wati ngati osewera awo akufuna ndalama azipeza zigoli.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi MAFCO ku Chitowe ndipo wati timu yake yataya mipata yochuluka yomwe akanatha kupambana mmasewerowa.
"Tafanana mphamvu ndi MAFCO pa masewero omwe tikanatha kupambana, tinasewera bwino mphindi zonse koma tinakanika kupeza zigoli nde ngati sikugoletsa ndekuti mufanana mphamvu ngati simunachinyitsenso." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachinayi pomwe ili ndi mapointsi okwana 40 pa masewero 23 omwe yasewera. Lolemba, iwo akumana ndi Mighty Mukuru Wanderers.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores