Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Majido
2023 FIFA WOMEN'S WORLD CUP CHAMPIONS! ππͺπΈ
Spain have won the Women's World Cup after beating England 1-0! ποΈπͺπΈ
πͺπΈ A brilliant performance from La Roja who win their first major honour.
2 - 1 big Bullets
"NDI NTCHITO YAKE" - NYAMBOSE WAKANA KUKWEZA NYASULU MU MTENGO
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, anakanika kuyamikira goloboyi wa timu yake, Innocent Nyasulu, atachotsa mapenate awiri mmasewero omwe anagonjetsa Dedza Dynamos 2-0 ponena kuti ndi ntchito yake.
Nyambose anati chipambano cha timuyi chinabwera kudzera mu kulimbikira kwa ntchito zake ndipo Nyasulu monga wapagolo amayenera kugwiranso ntchito yake.
"Yah ndi mnyamata wabwino ndipo amatithandiza kwambiri, kuchotsa mapenate awiri ndi chinthu cha mtengo wapatali koma ngati amakhala pamene paja ndekuti ndi ntchito yake, ndife odala poti tili naye." Anatero Nyambose.
Nyasulu tsopano wachotsa mapenate asanu mu chaka chokha chino mu ligi ya TNM ndipo anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mmasewerowa kachisanunso mu ligi ya chaka chino.
Tigers tsopano yafika pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligiyi.
"TATEMPHA AKULUAKULU AKAMBURANE NDI OSEWERA PA OKHA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati wapempha kuti akuluakulu atimuyi ayankhulane ndi osewera atimuyi pa zimene zikuvuta kutsatira kusachita bwino angakhale kuti akumasewera bwino mmasewero awo.
Kananji amayankhula izi pomwe timu yake inagonja 1-0 pakhomo ndi timu ya Moyale Barracks loweruka ndipo yataya mapointsi ochuluka mmasewero awo angakhale kuti anapeza mipata yochuluka.
Koma Kananji wati izi ndi zodabwitsa ndipo mwina pali vuto kuti anyamata ake asamapeze zigoli.
"Izi ndi zodabwitsa ndipo nzosowetsa kuti tiziti chani chifukwa chilichonse tikupanga koma anyamata akukanika kugoletsa nchifukwa chake tapempha akuluakulu atimuyi kuti ayankhulane ndi osewera kwa okha mwina atha kumatiopa." Anatero Kananji.
Kutsatira kugonjako, Eagles ili pa nambala 15 ndi mapointsi 17 pamasewero 18 a mu ligi ya TNM.
MANYOZO WAYAMBA KU MPIRA MMUDZI MWATHU
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Alfred Manyozo Jr, wayamba kugwira ntchito mongothandizira ku bungwe la Mpira mmudzi Mwathu pomwe akudikilira nkhani yake yomwe anamuyimitsira kutimuyi.
Manyozo anaimitsidwa ku Wanderers pomwe ochemerera ankafuna kumumenya komanso nkhani zoti samayankhula bwino osewera ena kutimuyi ndipo patha masabata odutsa anayi chimuimitsireni.
Izi zachititsa katswiriyu kuti azikangothandizira ku bungwe losula luso la ana achisodzera la Mpira Mmudzi Mwathu koma mwaulere.
Manyozo ndi yekha amene anayamba kutumikira timuyi kalekale pomwe anafika ku Nyerere mu zaka 15 zapitazo koma wakhala akulandira chitsonzo chachikulu ndi ochemerera atimuyi.
BIBI IKUWINA
KHUDA WAGOLETSANSO KUTI TIMU YAKE ITENGE CHIKHO
Katswiri wa timu ya Flames, Khuda Muyaba, wagoletsanso chigoli china chomwe chathandizira timu yake kukhala akatswiri a mpikisano wa October tournament pomwe anathandizira timu yake kupambana 2-1 ndi timu ya Hutteen ku Syria lachisanu.
Muyaba anamwetsa chigoli chokongola kwambiri kuti atengere zigoli zake mu mpikisanowu kufikira zinayi ndipo wakhala katswiri omwetsa zigoli zambiri mu mpikisanowu.
Iyi ndi sabata yoyamba kukhala mdzikolo koma Khuda waonetsa kale kukatswiri pomwe matimu akukonzekera za kuyamba kwa ligi yawo.
Pambali pogoletsa zigolizi iye wathandiziranso zigoli zina ziwiri mu mpikisanowu.
CHAWANANGWA WAONJEZERA MGWIRIZANO KU ZANACO
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, waonjezera mgwirizano wake ndi timu yaku Zambia ya Zanaco pomwe dzulo wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi.
Kawonga anapita kutimuyi chaka chatha pomwe anasaina mgwirizano wa chaka chimodzi kuchokera ku timu ya Silver Strikers ndipo timuyi yakhutitsidwa ndi kaseweredwe kake.
Matimu ambiri aku South Africa anayamba kudyerera maso pa katswiriyu atasewera mwapamwamba ku mpikisano wa COSAFA Cup ndi Flames pomwe anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa onse.
Iye wapatsidwa nambala 10 kukweza chikhulupiliro pa onse a kutimuyi ndipo akhalabe mpaka 2025 kutimuyi.
SULUMBA WAPITA KU KUWAIT
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Muhammad Sulumba, wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timu ya mdziko la Kuwait yotchedwa Sulaibikhat Sporting Club kuchoka mdziko la Bahrain komwe amasewera.
Katswiriyu watsimikiza poyankhula ndi tsamba la Wa Ganyu pomwe wati ndi wokondwa ndi chikhulupiliro chimene timuyi yaika pa katswiriyu ndipo ayesetsa kubwenzera zabwino kwa iye.
"Izi ndi zina zinanso, ndikuthokoza Mulungu kamba ka izi. Awa akhala ali maloto anga ndipo timuyi yandipatsa chikhulupiliro chambiri ndipo ndikuyenera kubwenzera zabwino pa chikhulupiliro chimenechi." Iye anatero pouza tsamba la Wa Ganyu.
Mwa zina, timuyi yamusankha ngati wachiwiri kwa mtsogoleri watimuyi, K5 million pomwe amasaina, K5 million akamuika pa chithunzi mu zinthu zawo, K4 million ngati ndalama ya pamwezi komanso galimoto yoyendera.
Sulaibikhat imasewera mu ligi yaying'ono ya ku Kuwait ndipo ikuyamba masewero pa 31 August ozigulira malo mu ligi yaikulu mdzikomo.
Olosera 5 agawana ndalama zoposa K10,000 atalosera bwino mwaulere masewero osachepera 10 sabata yatha pa website ya Owinna.com.
Congrats Luwiji, Manuel, Tiago, Xavier & Dami π
2-1
BANGWE YATENGA MKANDAWIRE
Timu ya Bangwe All Stars yalengeza kuti yatenga mphunzitsi wakale watimu ya Scorchers, Abel Mkandawire, kuti aphunzitse timuyi kwa miyezi isanu ndi umodzi ikudzayi.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lero pomwe yati Joseph Kamwendo ndi yemwe akhale wachiwiri kwa mphunzitsiyu.
Bangwe ili pa nambala 12 mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi okwana 18 pa masewero 17 omwe yasewera.
Ayitha koma ndawa coach anampeza afam e ay sakuyenela utelo akhoza umutenga
CHAMPIONS!
π¨Manchester City have won the UEFA Super Cup after beating Sevilla 5-4 on penalties following a 1-1 draw in Athens.
Quem leva tnm ja nao sei.
Otenga league sakudziwika komano, tibapatsa ali pamwambawa...
LWEMBA WAPEPESA KWA TIMU YAKE NDI OYIMBIRA
Mtsogoleri wa timu ya Chitipa United, Chris Lwemba, wapepesa kamba ka mkhalidwe lomwe anaonetsa pa masewero omwe timuyi inagonja 1-0 ndi Dedza Dynamos sabata yatha pomwe analandira kalata yofiira kamba kokwiya ndi ganizo la oyimbira.
Lwemba wati iye monga mtsogoleri amayenera kukhala chitsanzo kwa osewera anzake ndipo wati osewera ndi masapota atimuyi amukhululukire kamba ka mkhalidwewu.
Iye wapepesanso kwa Chidziwitso Simbi yemwe ankayimbira masewerowa kamba komugwiragwira pokwiya ndi penate yomwe oyimbirayu anapereka kwa Dedza.
Katswiriyu sapezeka mmasewero omwe timuyi ikukumana ndi Mighty Mukuru Wanderers kumapeto a sabata ino.
0 2
KHUDA WADYA WANI KU SYRIA
Katswiri wa timu ya Flames, Khuda Muyaba, wamwetsanso chigoli lero ndi kuthandizira china pomwe timu ya Tishreen yagonjetsa Al Hilal 4-1 ku Syria.
Muyaba anagoletsa chigoli chake mchigawo choyamba ndipo zigoli zina zachoka kwa Al-Laith Ali, Mustafa Billona ndi Claude Ike.
Katswiriyu tsopano wagoletsa zigoli zitatu ndi kuthandizira zigoli ziwiri mmasewero awiri oyambilira omwe wasewera mdzikoli mmasiku awiri.
FAM YATSEKA MABWALO A CIVO NDI MZUZU
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi, latseka mabwalo a Mzuzu ndi Civo kuti asachititsenso masewero aliwonse kamba koti salibwino.
Bungweli latulutsa kalata lachitatu yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Alfred Gunda, pomwe yati mabwalowa akusowekera zinthu zina zomwe zikupereka chiopsezo ku osewera.
Chiyambireni ligi ya chaka chino, aphunzitsi awiri, Peter De Jongh ndi Mark Harrison, akhala akudandaula ndi mmene bwaloli lilili ndipo FAM yapanga chiganizo chotseka bwaloli. Bwaloli linachititsanso masewero lachitatu lomweli amu ligi ya TNM.
Matimu a Civo United, Kamuzu Barracks, Extreme FC, Moyale Barracks ndi Ekwendeni Hammers ndi omwe akhudzidwa ndi kutseka kwa mabwalowa pomwe amagwiritsa ntchito ngati pakhomo pawo.
Nomar oyeee:
TODAYS LINE UP
IDANA WAPITA KU ZAMBIA
Katswiri wa Flames, Chimwemwe Idana, wafika mdziko la Zambia komwe zamveka kuti apita kutimu ya Kabwe Warriors ya mdzikomo.
Idana anatumikira timu ya Silver Strikers mchigawo choyamba cha ligi ya chaka chino koma mgwirizano wake wa pangongole kuchokera ku timu ya Mbeya City ndi Silver unatha.
Silver yakanika kugula katswiriyu kamba koti matimuwa sanamvane mtengo ndipo Mbeya ikutumizanso katswiriyu pa ngongole.
Tsatanetsatane wa nkhaniyi tikhale tikukupatsirani mu nkhani zathu zotsatira.
MOYALE YADYA K9 MILLION KU ZIMBABWE
Timu ya Moyale Barracks yapatsidwa ndalama zokwana K9 million kuchokera ku likulu la asilikali mdziko la Zimbabwe pomwe yagonjetsa asilikaliwa 1-0 dzulo kuti apambane chikhochi.
Timuyi inayimilira asilikali a mdziko uno pa mwambo okumbukira kuti asilikali a mdzikolo atha zaka 30 ndipo anaitana asilikali aku Malawi kuti awathandize kusangalala.
Mu masewerowa, Katswiri wakale wa Dwangwa United, Hassan Upindi, ndi yemwe anamwetsa chigoli chopambanira mmasewerowa.
Timuyi tsopano yatenga chikho ndiponso ndalama zokwana K9 million. Aka ndi kachiwiri timuyi kupita mdzikomo pomwe anapita mu 2019 komwe anakamaliza pa nambala yachiwiri.
OFFICIAL
Chelsea have announced the signing of Moises Caicedo from Brighton for a British record Β£115 million.
The Blues unveiled their latest signing in a statement on Monday.
The midfielder signed an eight-year deal that will see him stay at Stamford Bridge until 2031, plus the option of an extra year.
AARON WAPANIDWA NDI ZENERA
Katswiri wa timu ya CIvo, Lloyd Aaron, akadalibe katswiri watimuyi pomwe palibe timu iliyonse yomwe yamusaina katswiriyu mpaka msika wogula ndi kugulitsa osewera watsekedwa usiku wa dzulo.
Aaron anali ndi khumbo lotumikira ku Mighty Mukuru Wanderers koma timuyi inakanika kumvana ndi Civo pa mtengo wa K15 million yomwe imafunika pa katswiriyu.
Silver Strikers inalowanso m'bwalo pomwe inaika K7.5 million pa katswiriyu koma Civo inakana ndipo mochedwa inaika K10 million koma Aaron sanayankhe pomwe akufunitsitsa kupita ku Blantyre.
Wanderers ndi timu imene ili ndi mwayi wasaina katswiriyu ngati akufunabe pomwe inatumiza kale pempho pa Mpira Connect losamutsa osewerayu koma pangongole ndipo atakambirana ndi Civo, katswiriyu atha kuoneka kutimuyi.
Iyo yakonza K2 million ya ngongoleyi komanso K300,000 ngati ndalama ya pamwezi ya katswiriyu yemwe anadziwika kwambiri ku COSAFA Cup ndi Flames.
DEAL DONE
Chitipa United has signed Dedza Dynamos' goalkeeper, Andrew Ntimkulu, on a 5 month loan deal.
Both parties have confirmed the development and goalkeeper may be in the team's squad for the first against Mighty Mukuru Wanderers on Saturday.
KHUDA WAMWETSA KALE ZIWIRI
Katswiri osewera kutsogolo mutimu ya Flames, Khuda Muyaba wayamba mwapamwamba kutimu yake yatsopano pomwe wagoletsa zigoli ziwiri pamasewero omwe Tishreen SC yagonjetsa Jebala 5-1 usiku wa lolemba.
Muyaba anathandizira chigoli choyamba pomwe nthawi yopumulira, timuyi imatsogola 2-0 koma anagoletsa chigoli chachitatu ndi chachinayi asanamutulutse.
Zigoli zina zatimuyi anagoletsa ndi Hamid Meadow, Ayman Akil komanso Kamel Kawaya.
TSACHE LAYENDA KU BLUE EAGLES
Timu ya Blue Eagles yachotsa ena mwa akuluakulu omwe amaphunzitsa kutimuyi pomwe akufuna kukonza zinthu kutsatira kusachita bwino kwa timuyi.
Timuyi yabweretsa Gabriel Chirwa yemwe azigwira ntchito ngati team manager kulowa mmalo mwa Ken Mponda yemwe wachosedwa paudindowu.
Ena mwa anthu omwe asunthidwa ndi monga Audlow Makonyola yemwe amagwira ntchito ngati Technical Director komanso wachiwiri kwa Mphunzitsi wamkulu Christopher Sibale ndipo m'malo mwake abweretsa Phillip Masiye komanso nkhope zina zachilendo.
Timuyi ili ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili panambala 14 ndimapointi 17 pamasewero 17 omwe timuyi yasewera.
NTOPWA YALIMBITSA TIMU YAWO
Timu ya Ntopwa Super Queens yalimbitsa timu yawo patsogolo pa mpikisano wa CAF Women's Champions league pomwe yasaina osewera atatu pangongole.
Mwina wake wa timuyi, Isaac Jomo Osman, watsimikiza za kubwera kwa Rose Kabzere kuchokera ku Ascent Academy, Linda Kasenda wa Civo United komanso Vanessa Chikupira kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets Ladies kuti alimbitse timuyi ku mpikisano umenewu.
Ntopwa ili mu gulu A ya mpikisanowu ndi matimu a Green Buffaloes yaku Zambia, Double Action Ladies yaku Botswana ndi Lesotho Defense Force ndipo mpikisanowu uyamba pa 30 August kufika pa 8 September.
π¨ Pep Guardiola has confirmed that Kevin De Bruyne will face 'three to four' months out with a serious hamstring injury.
Robert saizi bwanji sawumenyela ku bullets
DONE DEAL
Neymar Jr will join Al-Hilal on a two year deal worth almost β¬100M as per Fabrizio Romano.
He'll travel to Saudi for medical tests today.
π¨ππ π πππππ: Kepa Arrizabalaga has joined Real Madrid on loan until June 30, 2024.
AARON AKUTANI KU BLANTYRE?
Owinna ili ndi malipoti kuti katswiri wa timu ya Civo United, Lloyd Aaron, ali mu mzinda wa Blantyre pomwe watsala pang'ono kusaina mgwirizano ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers msika wa osewera usanatsekedwe.
Mmodzi a anthu aku timu ya Wanderers, watsimikiza kwa Mtolankhani wathu kuti Aaron wamvana chilichonse ndi timuyi ndipo Wanderers ikumalizitsa zomvana ndi Civo United.
Timu ya Civo United inati ikufuna ndalama zokwana K15 million pa Aaron koma Manoma akukambirana za kamtengo kakang'ono ndi timuyi.
Inenso wati Dennis Chembezi sasaina ndi Wanderers mmalo mwake akuzisakira malo ku timu Ina kunja kwa dziko lino.
Aaron anadziwika kwambiri kamba kosewera bwino ndi timu ya Flames kumpikisano wa COSAFA Cup mdziko la South Africa chaka chino ndipo Silver Strikers imamufunanso.
KUMWEMBE WABWERERA MU BWALO
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, akuyembekezeka kubwereranso pa bwalo la zamasewero sabata ino pomwe wapita ku chigawo chakumpoto pamodzi ndi timu yake.
Kumwembe anavulala masabata atatu apitawo pomwe anaziongolaongola patsogolo pa masewero awo ndi Silver Strikers ndipo tsopano wachira.
Katswiriyu ali ndi zigoli zisanu ndi ziwiri mu ligi ya chaka chino ndipo timu yake ikukakumana ndi Ekwendeni Hammers lachitatu isanakumane ndi Chitipa United loweruka.
"BOLA AKUNJA KUSIYANA NDI AKU MALAWI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wayankhula pa chifukwa chimene timuyi sikugulira osewera ngakhale kuti osewera ena ndi ovulala ponena kuti akuyang'ana akunja osati a mdziko muno.
Munthali amayankhula izi atatha masewero awo omwe anagonjetsa Extreme FC 3-0 ndipo tsopano akukonzeka zolowera ku Equatorial Guinea kukakumana ndi FC Dragon mu CAF Champions league. Iye wati osewera aku Malawi amasiyana ndi akunja choncho ndi chifukwa chake sanagule.
"Osewerawa sikuti timangotenga umafunika uikeko kena kake nde ngati athuwa akabwera amafunika tiwaphunzitse poti samafikira kupanga zomwe timafuna bola akunja amafikira kugwira ntchito." Anatero Munthali.
Iye wati timu yake ndi yokonzeka mmasewerowa ndipo akuyang'ana chipambano mu CAF. Bullets yafika pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM ndi mapointsi 34 pamasewero 17.
CHIRWA WAPEREKA ULEMU KWA CHITIPA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wadabwa komanso kupereka ulemu kwa timu ya Chitipa United ponena kuti ndi timu yabwino pomwe timu yake ya Dedza Dynamos inasewera ndi timuyi.
Chirwa anayankhula izi atatha masewerowa ndipo chigoli cha Clement Nyondo chinapambanitsa Dedza pamwamba pa Chitipa ya anyamata khumi. Chirwa anati Chitipa ndi timu yabwino.
"Masewero anali abwino kwambiri, Chitipa United ili ndi osewera abwino kwambiri ndipo ndi timu yabwino koma ife tinapeza mipata taiphonya mwa mwayi tinapeza penate koma Chitipa ngakhale anali ochepa inalimba ndi timu yabwino." Anatero Chirwa.
Timu ya Dedza yafika pa nambala 7 mu ligi kutsatira kupambanaku pomwe yatolera mapointsi 22 pa masewero 17 omwe yasewera.
"OYIMBIRA ANAKONZA KALE ZOTSATIRA" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald Mtetemera, wati oyimbira Chidziwitso Simbi, anakonzeratu zotsatira za masewero awo pomwe wati samafuna kuti Chitipa iwine mmasewero omwe yagonja 1-0 ndi Dedza Dynamos.
Mtetemera anayankhula atatha masewero atimuyi pomwe Dedza inapambanira penate yomwe Clement Nyondo anagoletsa ndipo Nginde wati sinali penate.
"Masewero anali abwino kwambiri, timasewera bwino koma ndine okhumudwa ndi oyimbira, mwina anakonza kale kuti tisapambane masewerowa. Tinayesetsa, anyamata anasewera bwino tinabwera kuti tisewere mpira koma oyimbira anakonza kale zawo." Anatero Mtetemera.
Timuyi inamaliza ndi osewera khumi pomwe Chris Lwemba analandira chikalata chofiira kamba kosalankhula bwino kwa oyimbira. Timuyi yafika pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi 32 mmasewero 17 ndipo isewera ndi Wanderers loweruka.
"NDIMAKANGOFUNSA KWA OYIMBIRA" - LWEMBA
Mtsogoleri wa timu ya Chitipa United, Chris Lwemba, wati ndi okhumudwa ndi oyimbira wa masewero awo ndi Dedza Dynamos, Chidziwitso Simbi, pomwe anapereka kalata yofiira kwa iye ngakhale kuti amakafunsa oyimbirayu pa chiganizo chake.
Lwemba wauza Mtolankhani wa tsamba lino kuti anali odabwa ndi penate yomwe inaperekedwa mmasewerowa ndipo iye amakafunsa monga mtsogoleri wa timu.
"Ndinakafunsa kamba koti sinali penate komanso ndine mtsogoleri nde mpamene amandipatsa chikalata chofiira." Iye anatero mu chingerezi.
Lwemba anavuta mpaka amakana kutuluka koma osewera anzake ndi akuluakulu atimuyi anachita kumugwira kuti atuluke mu bwaloli. Iye wakhala ofunikira pomwe wasankhidwa kuti wasewera bwino mmasewero anayi ndipo tsopano sapezeka mmasewero atimuyi ndi Mighty Mukuru Wanderers lowerukali.
"PENATE YABODZA IJA YATILUZITSA" - BUNYA
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Extreme FC, Andrew Bunya, wati timu yake inagonja masewero awo kamba ka penate imene oyimbira Mayamiko Kanjere anapereka kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets lamulungu.
Bunya amayankhula izi atatha masewero omwe inagonja 3-0 ndipo anati oyimbira ndi yemwe anapangitsa kuti agonje.
"Mukunena penate yabodza ija, goloboyi anagwira mpira bwinobwino koma akuimba penate, zimenezo ndi zimene zatipangitsa kuti tichinyitse zigoli zambiri. Mchigawo choyamba sitimasewera bwino koma titabwera timasewera bwino koma penate ija inachotsa osewera mu game." Anatero Bunya.
Timuyi yalemba Bunya kamba koti inapezeka olakwa pogwiritsa ntchito mphunzitsi wopanda mapepala oyenerera. Extreme ili pa nambala 16 ndi mapointsi 10 pa masewero 17.
KELVIN KANANJI
Professional running of league affairs
Timu ya Civo United yasaina katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Harry Nyirenda, kuti akatumikire timuyi mu chigawo chachiwiri.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lolemba ndipo katswiriyu wapita kutimuyi pomwe anathetsa mgwirizano wake ndi timu ya Ekwendeni Hammers komwe wasewerako zaka ziwiri.
Mighty mukuru wanderers
EXTREME YALIMBITSA TIMU YAWO
Timu ya Extreme FC yasaina anyamata asanu ndi mmodzi (6) pomwe akufuna kumenyera nkhondo kuti akhalebe mu ligi ya TNM chaka chino.
Timuyi yatenga osewera awiri akale a Silver Strikers, Foster Bitoni ndi Mphatso Dzongololo mwaulere pomwe analibe timu Ina iliyonse.
Iwo atenganso anyamata ena anayi ndipo onse ndi awa:
βοΈFoster Bitoni (ulere) βοΈ Mphatso Dzongololo (Ulere) βοΈWillard Dickson (Civo) βοΈStephano John (Villa FC) βοΈJafallie John (Silver Reserve LOAN) βοΈWakisa Mwakifuna (Karonga United LOAN)
Source: Extreme FC | Zodiak
MAWULE MOTO PASOGOLO