KHUDA WADYA WANI KU SYRIA
Katswiri wa timu ya Flames, Khuda Muyaba, wamwetsanso chigoli lero ndi kuthandizira china pomwe timu ya Tishreen yagonjetsa Al Hilal 4-1 ku Syria.
Muyaba anagoletsa chigoli chake mchigawo choyamba ndipo zigoli zina zachoka kwa Al-Laith Ali, Mustafa Billona ndi Claude Ike.
Katswiriyu tsopano wagoletsa zigoli zitatu ndi kuthandizira zigoli ziwiri mmasewero awiri oyambilira omwe wasewera mdzikoli mmasiku awiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores