KHUDA WAGOLETSANSO KUTI TIMU YAKE ITENGE CHIKHO
Katswiri wa timu ya Flames, Khuda Muyaba, wagoletsanso chigoli china chomwe chathandizira timu yake kukhala akatswiri a mpikisano wa October tournament pomwe anathandizira timu yake kupambana 2-1 ndi timu ya Hutteen ku Syria lachisanu.
Muyaba anamwetsa chigoli chokongola kwambiri kuti atengere zigoli zake mu mpikisanowu kufikira zinayi ndipo wakhala katswiri omwetsa zigoli zambiri mu mpikisanowu.
Iyi ndi sabata yoyamba kukhala mdzikolo koma Khuda waonetsa kale kukatswiri pomwe matimu akukonzekera za kuyamba kwa ligi yawo.
Pambali pogoletsa zigolizi iye wathandiziranso zigoli zina ziwiri mu mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores