CHIRWA WAPEREKA ULEMU KWA CHITIPA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wadabwa komanso kupereka ulemu kwa timu ya Chitipa United ponena kuti ndi timu yabwino pomwe timu yake ya Dedza Dynamos inasewera ndi timuyi.
Chirwa anayankhula izi atatha masewerowa ndipo chigoli cha Clement Nyondo chinapambanitsa Dedza pamwamba pa Chitipa ya anyamata khumi. Chirwa anati Chitipa ndi timu yabwino.
"Masewero anali abwino kwambiri, Chitipa United ili ndi osewera abwino kwambiri ndipo ndi timu yabwino koma ife tinapeza mipata taiphonya mwa mwayi tinapeza penate koma Chitipa ngakhale anali ochepa inalimba ndi timu yabwino." Anatero Chirwa.
Timu ya Dedza yafika pa nambala 7 mu ligi kutsatira kupambanaku pomwe yatolera mapointsi 22 pa masewero 17 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores