TSACHE LAYENDA KU BLUE EAGLES
Timu ya Blue Eagles yachotsa ena mwa akuluakulu omwe amaphunzitsa kutimuyi pomwe akufuna kukonza zinthu kutsatira kusachita bwino kwa timuyi.
Timuyi yabweretsa Gabriel Chirwa yemwe azigwira ntchito ngati team manager kulowa mmalo mwa Ken Mponda yemwe wachosedwa paudindowu.
Ena mwa anthu omwe asunthidwa ndi monga Audlow Makonyola yemwe amagwira ntchito ngati Technical Director komanso wachiwiri kwa Mphunzitsi wamkulu Christopher Sibale ndipo m'malo mwake abweretsa Phillip Masiye komanso nkhope zina zachilendo.
Timuyi ili ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili panambala 14 ndimapointi 17 pamasewero 17 omwe timuyi yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores