MOYALE YADYA K9 MILLION KU ZIMBABWE
Timu ya Moyale Barracks yapatsidwa ndalama zokwana K9 million kuchokera ku likulu la asilikali mdziko la Zimbabwe pomwe yagonjetsa asilikaliwa 1-0 dzulo kuti apambane chikhochi.
Timuyi inayimilira asilikali a mdziko uno pa mwambo okumbukira kuti asilikali a mdzikolo atha zaka 30 ndipo anaitana asilikali aku Malawi kuti awathandize kusangalala.
Mu masewerowa, Katswiri wakale wa Dwangwa United, Hassan Upindi, ndi yemwe anamwetsa chigoli chopambanira mmasewerowa.
Timuyi tsopano yatenga chikho ndiponso ndalama zokwana K9 million. Aka ndi kachiwiri timuyi kupita mdzikomo pomwe anapita mu 2019 komwe anakamaliza pa nambala yachiwiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores