KHUDA WAMWETSA KALE ZIWIRI
Katswiri osewera kutsogolo mutimu ya Flames, Khuda Muyaba wayamba mwapamwamba kutimu yake yatsopano pomwe wagoletsa zigoli ziwiri pamasewero omwe Tishreen SC yagonjetsa Jebala 5-1 usiku wa lolemba.
Muyaba anathandizira chigoli choyamba pomwe nthawi yopumulira, timuyi imatsogola 2-0 koma anagoletsa chigoli chachitatu ndi chachinayi asanamutulutse.
Zigoli zina zatimuyi anagoletsa ndi Hamid Meadow, Ayman Akil komanso Kamel Kawaya.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores