"NDIMAKANGOFUNSA KWA OYIMBIRA" - LWEMBA
Mtsogoleri wa timu ya Chitipa United, Chris Lwemba, wati ndi okhumudwa ndi oyimbira wa masewero awo ndi Dedza Dynamos, Chidziwitso Simbi, pomwe anapereka kalata yofiira kwa iye ngakhale kuti amakafunsa oyimbirayu pa chiganizo chake.
Lwemba wauza Mtolankhani wa tsamba lino kuti anali odabwa ndi penate yomwe inaperekedwa mmasewerowa ndipo iye amakafunsa monga mtsogoleri wa timu.
"Ndinakafunsa kamba koti sinali penate komanso ndine mtsogoleri nde mpamene amandipatsa chikalata chofiira." Iye anatero mu chingerezi.
Lwemba anavuta mpaka amakana kutuluka koma osewera anzake ndi akuluakulu atimuyi anachita kumugwira kuti atuluke mu bwaloli. Iye wakhala ofunikira pomwe wasankhidwa kuti wasewera bwino mmasewero anayi ndipo tsopano sapezeka mmasewero atimuyi ndi Mighty Mukuru Wanderers lowerukali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores