"NDI NTCHITO YAKE" - NYAMBOSE WAKANA KUKWEZA NYASULU MU MTENGO
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, anakanika kuyamikira goloboyi wa timu yake, Innocent Nyasulu, atachotsa mapenate awiri mmasewero omwe anagonjetsa Dedza Dynamos 2-0 ponena kuti ndi ntchito yake.
Nyambose anati chipambano cha timuyi chinabwera kudzera mu kulimbikira kwa ntchito zake ndipo Nyasulu monga wapagolo amayenera kugwiranso ntchito yake.
"Yah ndi mnyamata wabwino ndipo amatithandiza kwambiri, kuchotsa mapenate awiri ndi chinthu cha mtengo wapatali koma ngati amakhala pamene paja ndekuti ndi ntchito yake, ndife odala poti tili naye." Anatero Nyambose.
Nyasulu tsopano wachotsa mapenate asanu mu chaka chokha chino mu ligi ya TNM ndipo anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mmasewerowa kachisanunso mu ligi ya chaka chino.
Tigers tsopano yafika pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores