NTOPWA YALIMBITSA TIMU YAWO
Timu ya Ntopwa Super Queens yalimbitsa timu yawo patsogolo pa mpikisano wa CAF Women's Champions league pomwe yasaina osewera atatu pangongole.
Mwina wake wa timuyi, Isaac Jomo Osman, watsimikiza za kubwera kwa Rose Kabzere kuchokera ku Ascent Academy, Linda Kasenda wa Civo United komanso Vanessa Chikupira kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets Ladies kuti alimbitse timuyi ku mpikisano umenewu.
Ntopwa ili mu gulu A ya mpikisanowu ndi matimu a Green Buffaloes yaku Zambia, Double Action Ladies yaku Botswana ndi Lesotho Defense Force ndipo mpikisanowu uyamba pa 30 August kufika pa 8 September.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores