"BOLA AKUNJA KUSIYANA NDI AKU MALAWI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wayankhula pa chifukwa chimene timuyi sikugulira osewera ngakhale kuti osewera ena ndi ovulala ponena kuti akuyang'ana akunja osati a mdziko muno.
Munthali amayankhula izi atatha masewero awo omwe anagonjetsa Extreme FC 3-0 ndipo tsopano akukonzeka zolowera ku Equatorial Guinea kukakumana ndi FC Dragon mu CAF Champions league. Iye wati osewera aku Malawi amasiyana ndi akunja choncho ndi chifukwa chake sanagule.
"Osewerawa sikuti timangotenga umafunika uikeko kena kake nde ngati athuwa akabwera amafunika tiwaphunzitse poti samafikira kupanga zomwe timafuna bola akunja amafikira kugwira ntchito." Anatero Munthali.
Iye wati timu yake ndi yokonzeka mmasewerowa ndipo akuyang'ana chipambano mu CAF. Bullets yafika pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM ndi mapointsi 34 pamasewero 17.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores