"OYIMBIRA ANAKONZA KALE ZOTSATIRA" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald Mtetemera, wati oyimbira Chidziwitso Simbi, anakonzeratu zotsatira za masewero awo pomwe wati samafuna kuti Chitipa iwine mmasewero omwe yagonja 1-0 ndi Dedza Dynamos.
Mtetemera anayankhula atatha masewero atimuyi pomwe Dedza inapambanira penate yomwe Clement Nyondo anagoletsa ndipo Nginde wati sinali penate.
"Masewero anali abwino kwambiri, timasewera bwino koma ndine okhumudwa ndi oyimbira, mwina anakonza kale kuti tisapambane masewerowa. Tinayesetsa, anyamata anasewera bwino tinabwera kuti tisewere mpira koma oyimbira anakonza kale zawo." Anatero Mtetemera.
Timuyi inamaliza ndi osewera khumi pomwe Chris Lwemba analandira chikalata chofiira kamba kosalankhula bwino kwa oyimbira. Timuyi yafika pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi 32 mmasewero 17 ndipo isewera ndi Wanderers loweruka.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores