"TATEMPHA AKULUAKULU AKAMBURANE NDI OSEWERA PA OKHA" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati wapempha kuti akuluakulu atimuyi ayankhulane ndi osewera atimuyi pa zimene zikuvuta kutsatira kusachita bwino angakhale kuti akumasewera bwino mmasewero awo.
Kananji amayankhula izi pomwe timu yake inagonja 1-0 pakhomo ndi timu ya Moyale Barracks loweruka ndipo yataya mapointsi ochuluka mmasewero awo angakhale kuti anapeza mipata yochuluka.
Koma Kananji wati izi ndi zodabwitsa ndipo mwina pali vuto kuti anyamata ake asamapeze zigoli.
"Izi ndi zodabwitsa ndipo nzosowetsa kuti tiziti chani chifukwa chilichonse tikupanga koma anyamata akukanika kugoletsa nchifukwa chake tapempha akuluakulu atimuyi kuti ayankhulane ndi osewera kwa okha mwina atha kumatiopa." Anatero Kananji.
Kutsatira kugonjako, Eagles ili pa nambala 15 ndi mapointsi 17 pamasewero 18 a mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores