MANYOZO WAYAMBA KU MPIRA MMUDZI MWATHU
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Alfred Manyozo Jr, wayamba kugwira ntchito mongothandizira ku bungwe la Mpira mmudzi Mwathu pomwe akudikilira nkhani yake yomwe anamuyimitsira kutimuyi.
Manyozo anaimitsidwa ku Wanderers pomwe ochemerera ankafuna kumumenya komanso nkhani zoti samayankhula bwino osewera ena kutimuyi ndipo patha masabata odutsa anayi chimuimitsireni.
Izi zachititsa katswiriyu kuti azikangothandizira ku bungwe losula luso la ana achisodzera la Mpira Mmudzi Mwathu koma mwaulere.
Manyozo ndi yekha amene anayamba kutumikira timuyi kalekale pomwe anafika ku Nyerere mu zaka 15 zapitazo koma wakhala akulandira chitsonzo chachikulu ndi ochemerera atimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores