Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
MANOMA NDI MABANKER AKAGOGODANSO KU CIVO
Matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Silver Strikers alowa nnawo mu gulu lofuna katswiri watimu ya Civo United, Lloyd Aaron, kuti amugule.
Matimuwa adzidzimuka ataona kuti Bullets yapempha Civo kuti iwagulitse katswiriyu pomwe iwo ndi omwe anaonetsa chidwi chachikulu chotenga katswiriyu wa Flamesyu.
Izi zipangitsa kuti malonda a katswiriyu avute pomwe Civo iziyendera tsopano komwe akhuthula ndalama zambiri ndipo katswiriyu anali pa K15 million mphamvu ya kwacha isanagwe.
AARON WAPANIDWA NDI ZENERA
Katswiri wa timu ya CIvo, Lloyd Aaron, akadalibe katswiri watimuyi pomwe palibe timu iliyonse yomwe yamusaina katswiriyu mpaka msika wogula ndi kugulitsa osewera watsekedwa usiku wa dzulo.
Aaron anali ndi khumbo lotumikira ku Mighty Mukuru Wanderers koma timuyi inakanika kumvana ndi Civo pa mtengo wa K15 million yomwe imafunika pa katswiriyu.
Silver Strikers inalowanso m'bwalo pomwe inaika K7.5 million pa katswiriyu koma Civo inakana ndipo mochedwa inaika K10 million koma Aaron sanayankhe pomwe akufunitsitsa kupita ku Blantyre.
Wanderers ndi timu imene ili ndi mwayi wasaina katswiriyu ngati akufunabe pomwe inatumiza kale pempho pa Mpira Connect losamutsa osewerayu koma pangongole ndipo atakambirana ndi Civo, katswiriyu atha kuoneka kutimuyi.
Iyo yakonza K2 million ya ngongoleyi komanso K300,000 ngati ndalama ya pamwezi ya katswiriyu yemwe anadziwika kwambiri ku COSAFA Cup ndi Flames.
AARON AKUTANI KU BLANTYRE?
Owinna ili ndi malipoti kuti katswiri wa timu ya Civo United, Lloyd Aaron, ali mu mzinda wa Blantyre pomwe watsala pang'ono kusaina mgwirizano ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers msika wa osewera usanatsekedwe.
Mmodzi a anthu aku timu ya Wanderers, watsimikiza kwa Mtolankhani wathu kuti Aaron wamvana chilichonse ndi timuyi ndipo Wanderers ikumalizitsa zomvana ndi Civo United.
Timu ya Civo United inati ikufuna ndalama zokwana K15 million pa Aaron koma Manoma akukambirana za kamtengo kakang'ono ndi timuyi.
Inenso wati Dennis Chembezi sasaina ndi Wanderers mmalo mwake akuzisakira malo ku timu Ina kunja kwa dziko lino.
Aaron anadziwika kwambiri kamba kosewera bwino ndi timu ya Flames kumpikisano wa COSAFA Cup mdziko la South Africa chaka chino ndipo Silver Strikers imamufunanso.
CIVO IKUFUNA K15 MITA, IDZADYAPONSO AKADZAGULITSIDWA KUNJA
Timu ya Civo United ikufuna ndalama yokwana K15 million pa mnyamata wawo, Lloyd Aaron, pomwe matimu ambiri mdziko muno akumufuna.
Izi zadza pomwe katswiriyu analemba kalata yopempha timuyi kupanga zokambirana ndi matimu ena ndipo timuyi sinamutsekereze ndipo yati Aki ndi ufulu ochoka.
Ndipo timuyi yati matimu adziwe kuti Aaron ali ndi mgwirizano wofika mu 2025 ndipo iwo adzafunapo K15 million pa katswiriyu. Ngati timu idzamugulitse kunja, Civo United idzadyaponso K15 pa K100 ina iliyonse.
Matimu a Silver Strikers komanso Mighty Mukuru Wanderers ndi omwe afikira timuyi kufuna zintchito za katswiriyu kuti awathandize mu chigawo chachiwiri. Aaron wadziwika kwambiri pomwe anali ndi Flames ku COSAFA ndipo ali ndi zaka 22.
CHIMANGO KAYIRA SALUTES ARNOLD
Former Flames defending midfielder, Chimango Kayira, has saluted the current defending midfielder of the team, Lloyd Arnold, after his stellar performance in his dream competitive debut with the team on Thursday as they defeated Zambia 1-0 at the COSAFA Cup.
Arnold was brilliant in the game which has made him earn praises from sports spectators in the country and Kayira says the Civo United player has a bright future.
"He executed his duties without fear The future looks bright. We hope he will grow and build confidence from such marvelous displays." Said Kayira.
Arnold made his first appearance with the Flames in a friendly against Mozambique last month and the Zambia match was his first in a recognized competition and played the whole minutes.