Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TIMU NGATI WANDERERS IMAFUNIKIRA CHIKHO CHAKA CHILICHONSE" - KUMWEMBE
Katswiri watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, wati sakuyang'ana kuti akupeza zigoli motani koma kuti timu izichita bwino pomwe wati timu yaikulu ngati Wanderers sifunika kutuluka opanda chikho.
Kumwembe anayankhula izi atasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mmasewero omwe Wanderers yagonjetsa Karonga United 2-1 ndipo iye anamwetsa zigoli ziwiri. Iye anati kuvulala ndi kumene kunamusokoneza koma amadziwa kuti abwereramo.
"Sindimayang'ana kuti ndifike pati koma kukhala kumbali yoluza zimawawa nde mmene masapota amakuwira zinandilimbikitsa kuti ndipeze zigolizi. Kuvulala kunandisokoneza ndakhala mwezi osamenya mpira komabe ndizitolera bwinobwino." Anatero Kumwembe.
Katswiriyu wakhala pafupifupi miyezi itatu osagoletsa chigoli chilichonse mu ligi ya TNM koma tsopano ali ndi zigoli 9 ndipo akuchepekedwa ndi zigoli zinayi kuti amupeze Clement Nyondo.
#Tawonga2023
"KUMWEMBE SANAMALIZE KUTIGWIRITSA NTCHITO" - MPINGANJIRA
Mkulu watimu ya timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Roosevelt Mpinganjira, wati timu yawo sinathane ndi katswiri wawo Christopher Kumwembe pomwe amukaniza kuti apite kutimuyi ya Green Buffaloes yaku Zambia yomwe inamufuna.
Zinamveka kuti timu ya Buffaloes imafunitsitsa Kumwembe ndipo inalembera Wanderers ndipo timuyi inaika Kumwembe pa mtengo wa $80 million yomwe Buffaloes imafuna mtengowu utsitsidwe koma Manoma amakana.
Mpinganjira wati analandira kalata ndithu yochokera kutimuyi komatu iwo sali okonzeka kugulitsa Kumwembe.
"Kalata tinalandiradi koma tsopano sitinali okonzeka kumugulitsa Kumwembe chifukwa tinamugula kuti atigwirire ntchito ndipo ntchito akadzagwira tidzamulora kuti achoke." Mpinganjira anafotokoza.
Buffaloes inaona Kumwembe kutimu ya Flames pomwe anali ku COSAFA ndipo katswiriyu ali ndi zigoli zokwana zisanu ndi ziwiri mu ligi ya chaka chino.
KUMWEMBE WABWERERA MU BWALO
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, akuyembekezeka kubwereranso pa bwalo la zamasewero sabata ino pomwe wapita ku chigawo chakumpoto pamodzi ndi timu yake.
Kumwembe anavulala masabata atatu apitawo pomwe anaziongolaongola patsogolo pa masewero awo ndi Silver Strikers ndipo tsopano wachira.
Katswiriyu ali ndi zigoli zisanu ndi ziwiri mu ligi ya chaka chino ndipo timu yake ikukakumana ndi Ekwendeni Hammers lachitatu isanakumane ndi Chitipa United loweruka.
NOMA IKUFUNA K83 MILLION PA KUMWEMBE
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yati ikufuna ndalama yokwana K83 million pa mnyamata wawo, Christopher Kumwembe, kutimu yaku Zambia, Green Buffaloes yomwe ikufuna katswiriyu.
Mkulu watimuyi, Roosevelt Mpinganjira, watsimikiza zoti timuyi inalandira kalata kuchokera ku timu yaku Zambia imeneyi kuti akufuna katswiriyu atamuona ku mpikisano wa COSAFA Cup ku South Africa koma Manoma sali okonzekera kugulitsa osewerayu.
Koma malingana ndi malipoti a tsamba la Bola News, timu ya Wanderers inauza Buffaloes kuti ipereke ndalama yokwana $73 million yomwe ndi pafupifupi K83 million.
Kumwembe anagoletsa chigoli chimodzi ku COSAFA ndipo wamwetsa zigoli 7 mu masewero khumi omwe wasewera mu ligi ya chaka chino.
KUMWEMBE WAVULALA POMWE OSEWERA A FLAMES AKUVUTIKA
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, anakanika kusewera masewero atimu yake ndi Blue Eagles pomwe anavulala akupanga zoziongola masewerowa asanayambe.
Kumwembe anayikidwa kuti ayambe panja koma anachotsedwa pa ndandanda wa osewera kamba koti anavulala. Mulingo wa kuvulala kwake sunalengezedwe ndi timuyi.
Anthu ambiri adabwa ndi mmene osewera omwe anali ndi Flames ku COSAFA akuvulalira pomwe Robert Saizi anangosewera mphindi 24 pamasewero omwe Bangwe All Stars inalephera 1-1 ndi Ekwendeni Hammers.
Osewera ena omwe anali ndi Flames koma sakupezeka kamba kuvulala ndi Chimwemwe Idana ndi Patrick Macheso onse a Silver Strikers.
Pajatu anthu ananena kuti ma players akanapuma kaye
KUMWEMBE WAYAMBAPO
Katswiri wa Flames, Christopher Jacammah Kumwembe, wagoletsa chigoli chake choyamba pomwe dzulo wathandiza timuyi kupambana 2-0 ndi timu ya Seychelles ku mpikisano wa COSAFA ku South Africa.
Kumwembe anagoletsa chigoli chachiwiri mmasewerowa pomwe anamalizitsa mpira omwe Lanjesi Nkhoma anaumenya ndipo goloboyi wa Seychelles anauchotsa.
Awa anali masewero ake achitatu ndi timuyi pomwe anasewera masewero oyamba ndi Lesotho mmasewero aubale omwe anathera 1-1 ndipo anaseweranso mphindi makumi asanu ndi imodzi mmasewero oyamba ku mpikisanowu ndi Zambia.
Mmasewero a Seychelles, iye anasewera mphindi zonse koyamba ku timuyi. Chigoli china cha Flames anagoletsa ndi Lanjesi Nkhoma. Iye analinso ndi zigoli 7 mu ligi ya TNM ku Malawi.
Christopher kumwembe