SULUMBA WAPITA KU KUWAIT
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Muhammad Sulumba, wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timu ya mdziko la Kuwait yotchedwa Sulaibikhat Sporting Club kuchoka mdziko la Bahrain komwe amasewera.
Katswiriyu watsimikiza poyankhula ndi tsamba la Wa Ganyu pomwe wati ndi wokondwa ndi chikhulupiliro chimene timuyi yaika pa katswiriyu ndipo ayesetsa kubwenzera zabwino kwa iye.
"Izi ndi zina zinanso, ndikuthokoza Mulungu kamba ka izi. Awa akhala ali maloto anga ndipo timuyi yandipatsa chikhulupiliro chambiri ndipo ndikuyenera kubwenzera zabwino pa chikhulupiliro chimenechi." Iye anatero pouza tsamba la Wa Ganyu.
Mwa zina, timuyi yamusankha ngati wachiwiri kwa mtsogoleri watimuyi, K5 million pomwe amasaina, K5 million akamuika pa chithunzi mu zinthu zawo, K4 million ngati ndalama ya pamwezi komanso galimoto yoyendera.
Sulaibikhat imasewera mu ligi yaying'ono ya ku Kuwait ndipo ikuyamba masewero pa 31 August ozigulira malo mu ligi yaikulu mdzikomo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores