FAM YATSEKA MABWALO A CIVO NDI MZUZU
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi, latseka mabwalo a Mzuzu ndi Civo kuti asachititsenso masewero aliwonse kamba koti salibwino.
Bungweli latulutsa kalata lachitatu yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Alfred Gunda, pomwe yati mabwalowa akusowekera zinthu zina zomwe zikupereka chiopsezo ku osewera.
Chiyambireni ligi ya chaka chino, aphunzitsi awiri, Peter De Jongh ndi Mark Harrison, akhala akudandaula ndi mmene bwaloli lilili ndipo FAM yapanga chiganizo chotseka bwaloli. Bwaloli linachititsanso masewero lachitatu lomweli amu ligi ya TNM.
Matimu a Civo United, Kamuzu Barracks, Extreme FC, Moyale Barracks ndi Ekwendeni Hammers ndi omwe akhudzidwa ndi kutseka kwa mabwalowa pomwe amagwiritsa ntchito ngati pakhomo pawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores