CHAWANANGWA WAONJEZERA MGWIRIZANO KU ZANACO
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, waonjezera mgwirizano wake ndi timu yaku Zambia ya Zanaco pomwe dzulo wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi.
Kawonga anapita kutimuyi chaka chatha pomwe anasaina mgwirizano wa chaka chimodzi kuchokera ku timu ya Silver Strikers ndipo timuyi yakhutitsidwa ndi kaseweredwe kake.
Matimu ambiri aku South Africa anayamba kudyerera maso pa katswiriyu atasewera mwapamwamba ku mpikisano wa COSAFA Cup ndi Flames pomwe anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa onse.
Iye wapatsidwa nambala 10 kukweza chikhulupiliro pa onse a kutimuyi ndipo akhalabe mpaka 2025 kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores