Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"SITIMAMENYA NDI CRECK KOMA GULU" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati zotsatira za masewero atimu yake ndi Creck Sporting Club sizabwino poti amafunitsitsa atapambana koma vuto amamenya ndi osewera odutsa khumi ndi mmodzi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati chigoli chachiwiri cha anzawowa sichinali chabwinobwino..
"Anali masewero abwino kwambiri tasewera bwino ku mbali yathu koma zotsatira nde sizabwino komabe lero sitinasewere ndi osewera 11 koma timasewera ndi ambiti, chigoli chachiwiri chawo chija kaya poti kuona kwawo koma kumbali yanga sichimayenera kuloledwa." Anatero Mponda.
Iye wati timu yake ili ndi masewero aakulu patsogolo pawo ndi timu ya Civil Service United ndipo ndi mmene asewerera ndi Blue Eagles komanso Creck akukhulupilira kuti akachita bwino.
Timuyi ikadali pamwamba pomwe ili ndi mapointsi okwana 50 pa masewero 22 omwe asewera.
Takutumizirani nonse awiri ππ
"TIMAYENERA KUWINA MWA NJIRA ILIYONSE" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake imayenera kuwina mwanjira iliyonse mmasewero omwe amasewera ndi timu ya Silver Strikers komabe point imodzi ndi yofunikira kwa iwonso.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati timu yake inakonzekera zoti ipambane koma anakanika kumateteza zigoli zomwe anagoletsa.
"Anali masewero abwino kwambiri timayenera kupambana mwa njira iliyonse koma zativuta tangokwanitsa kufanana mphamvu kokha tivomereze kuti zatero koma chipambano ndi chomwe timafuna." Anatero Mtetemera.
Iye wati kulakwitsa komwe amachita pa masewero awowa akonza kuti tsopano mmasewero akudzawa ayambe kuchita bwino.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pa masewero 23 omwe yasewera poti yakwanitsa kupeza mapointsi okwana 32 mu ligiyi.
"NDIKUKHULUPILIRA KUTI TIDZACHITA BWINO NDI BULLETS" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wati akudziwa kuti masewero awo otsatira mu chikho cha Airtel Top 8 ndi FCB Nyasa Big Bullets adzakhala ovuta koma akonzekera bwino kuti adzachite bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa United 4-3 pa mapenate pomwe mmasewero onse awiri anathera 2-2 pa bwalo la Civo ndipo wati anali masewero ovuta pomwe kukonzekera kwawo kuti mchigawo choyamba adzagoletse zigoli zambiri sikunatheke.
Iye wati akudziwa kuti Bullets ndi timu yabwino koma timu iliyonse imafunitsitsa itafika mu ndime yotsiriza.
"Tikudziwa kuti adzakhala masewero ovuta kwambiri koma ndime ya matimu anayi imakhala yofunikira kwambiri ku timu iliyonse poti imafuna kufika mu ndime yotsiriza nde anyamata akudziwa mmene angachitire tikukhulupilira kuti tichita bwino." Anatero Kamanga.
Mu ndime ina ya matimu anayi ya Airtel Top 8, matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers adzak
"KB IDUTSA MOFEWA CHIFUKWA AMENYA KALE NDI YOVUTA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose, wafunira zabwino timu ya Kamuzu Barracks mu mpikisano wa Airtel Top 8 ndipo akukhulupilira kuti kwinako adutsa mofewa poti ovuta anali iwowo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-3 pa mapenate pomwe mu mphindi 90 anagonja 2-0 koma anafanana mphamvu 2-2 poti anapambana mmasewero oyambawo.
Iye anati, "Anali masewero abwino mapenate amapita kwa wina aliyense koma tiwayamikire a KB asewera bwino ndipo tiwafunire zabwino kungoti achita bwino afika patali poti amasewera ndi timu yovuta lero anawa ayi." Anatero Nyambose.
Iye anati anyamata ake anangogona pang'ono zomwe zinachititsa kuti apezetse zigoli zonse ndipo akakonza mavuto onse kuti achite bwino.
Zateremu, Kamuzu Barracks ikakumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ina ya mpikisanowu pomwe mmasewero ena, Silver Strikers ikukana ndi Mighty Mukuru Wanderers.
"IT'S SWEET TO DO IT AGAINST CITY RIVALS" - MPULULA
Mighty Tigers head coach, Leo Mpulula, says their win against Bangwe All Stars is a molare booster considering the current form of their rivals and also the fact that they were playing their rivals as it has set a clear path for the top 8 finish in the League.
He said this after sealing a 1-0 win at the Kamuzu Stadium and said it was sweet to win against Bangwe as the second round needs banking points in order to avoid relegation this season.
"It is indeed a sweet win when you do it against City rivals, Bangwe has really improved and are playing very well and this win is a molare booster and has given us confidence that we need to collect more points so that we remain in the League and also finish in the top 8." Said Mpulula.
He said his team dwells much on passing football hence their goal on Sunday was a build up of neat passes into the goal.
The Kaukau boys have moved up to 27 points from 23 games this season as they remain 1
"TIKUYENERA KUMAPAMBANA MASEWERO ONSE" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati kugonja kwawo ndi timu ya Mighty Tigers kwawaphunzitsa kuti asamalimbikire masewero aakulu be okha komanso azilimbikira pa masewero aliwonse mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Kamuzu lamulungu ndipo wati zinawavuta chifukwa amasewera ndi timu yoti akudziwana nayo kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri, timasewera ndi timu yodziwana nayo timakonzekerera bwalo limodzi koma zimachitika mu mpira basi tagonja." Anatero Kajawa.
Iye anati sangayankhule zambiri poti anyamata ake omwewo ndi omwe anakwanitsa kuchita bwino ndi Wanderers, Silver ndi Bullets ndipo ayesetsa kuti asuntheko kumunsi komwe ali popeza mapointsi ambiri.
Timuyi ili ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 23 omwe yasewera ndipo ili pa nambala 14 mu ligi ya TNM.
"TINAWATSEKERA MOMWE AMADUTSAMO" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Crespo Chimkwita, wati ndi wokondwa kuti timu yake yapeza chipambano pamwamba pa timu ya Mighty Mukuru Wanderers ndipo anadziwa kuti ayitsekere mmbali momwe anzawowa amadutsa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 pa bwalo la Karonga ndipo wati monga poti amasewera pakhomo iwowa amangoyenera kuti apeze chipambano.
"Ndife osangalala kwambiri ndipo chipambano chimenechi timachiyembekezera kwambiri komanso timadziwa kuti pakutha lero tifika pa nambala 7 nde tinali pakhomo pomwe abale athu onse analipo timayenera kupambana." Anatero Chimkwita.
Iye anatinso ayesetsa kuti akwanitse kumatolera mapointsi pa masewero omwe akusewera ndi cholinga choti adzathere pabwino ligiyi ikadzatha.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi 33 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligi chaka chino.
"SILINALI TSIKU LATHU" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake inayesetsa kupeza mipata yochuluka kuti mwina angathe kupeza chigoli komabe zawavuta poti tsiku silinali lawo basi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Karonga United pa bwalo la Karonga ndipo wati chigoli chomwe chinabwera mofulumira kwambiri ndi chomwe chinawasokonezanso.
"Tagonja tivomereze mutha kuona kuti tinachinyitsa mwansanga kwambiri koma tinayesetsa kuti mwina tingathe kubwenza tiwathokoze anyamata kuti asewera bwino koma silinali tsiku lathu basi." Anatero Mwase.
Iye wati timu yake siyitopa pomwe masewero asanu ndi atatu atsalawa ayesetsa kuti achite bwino poti mu mpira chilichonse chikhonza kuchitika.
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 44 pa masewero 22 omwe asewera pomwe akusiyana mapointsi asanu ndi imodzi ndi Silver Strikers.
"NDASANGALALA NDI MMENE TASEWERERA MCHIGAWO CHACHIWIRI" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati si zinthu zophweka kugoletsa zigoli zitatu ndi kupambana masewero mu chigawo chachiwiri cha ligi ndipo wati ndiwokondwa ndi mmene timu yake yasewerera mchigawo chachiwiri cha masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya FOMO FC 3-1 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati wasangalala kwambiri ndi chipambanochi.
"Anali masewero abwino kwambiri FOMO ndi timu yabwino ndipo yasewera bwino kwambiri komanso inayamba kugoletsa koma tinabwenza ndipo mchigawo chachiwiri tinawauza anyamata, asewera bwino kwambiri mpaka tapeza zigoli ndasangalala kwambiri." Anatero Mwansa.
Iye wati ayesetsa kuti ngakhale masewero azivuta chotere, timuyi izitolera mapointsi mu ligi kuti athere pabwino ligi ikamadzatha.
Zateremu timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi okwana 32 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligi.
"NDI KUGONJA KOPWETEKA KWAMBIRI" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Elvis Kafoteka, wati kugonja Kwa timu yake ndi Moyale Barracks ndi kopweteka kwambiri kamba koti kulakwitsa kwa okhaokha ndi kumene kwawapweteka kuti agonje chotere.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati anayesetsa kuti abweremo koma zinavuta mpake agonja.
"Tivomereze tagonja koma kugonja kopweteka kwambiri chifukwa timangolakwitsana tokhatokha mpaka kuchinyitsa zigoli zonsezo nde basi tibwerera tikakonze mavuto athu kuti tiyang'ane chitsogolo." Anatero Kafoteka.
Iye anati timu yake sakuyipatsa phuma lililonse pa masewero omwe yasewera poti akufuna kuti alimbikire chabe kuti apeze mapointsi poti anyamata ake ndi omwewa omwe akhala akuchita bwino.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi okwana 22 pa masewero 23 omwe yasewera mu
"LERO ZATIYENDERA KWAMBIRI" - IKWANGA
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City City Hammers, Kondwa Ikwanga, wati waona ubwino wogoletsa mofulumira pa masewero pomwe zawathandizira kuti ziwayendere mmasewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Baka City 0-4 pa bwalo la Karonga ndipo wati akufunitsitsa kuti akhale mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligiyi.
"Anali masewero abwino kwambiri tinayamba ndi kugoletsa chigoli cha msanga ndipo chatithandizira kuti tiwabalalitse anzathuwa nde lero taona ubwino wogoletsa mofulumira zatiyendera ndithu." Anatero Ikwanga.
Iye watinso alimbikira kuti atolere mapointsi ambiri pa masewero omwe atsalawa kuti adzathere pabwino ligiyi ikamadzatha.
Timuyi ili pa nambala yachitatu pomwe ili ndi mapointsi okwana 39 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligi ndipo yatsala ndi masewero asanu ndi amodzi.
"TINAKANIKA KUGWIRITSA NTCHITO MIPATA YATHU" - MZUNGA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Jimmy Mzunga, wayamikira osewera ake kuti anasewera bwino kwambiri mmasewero awo koma zangovuta kuti sanagwiritse ntchito mipata yomwe anapeza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Chitowe ndi timu ya Premier Bet Dedza Dynamos ndipo wati akanatha kuchita bwino ngati akanagoletsa mipata yomwe anapeza.
"Anali masewero abwino tasewera bwino kuyambira koyamba mpaka kumapeto tasunga mpira kwambiri koma mipata yomwe tinayipeza takanika kugoletsa, anyamata athu sanagwiritse ntchito mipatayi." Anatero Mzunga.
Iye wati mavuto omwe awona mmasewerowa abwerera kukakonza akabwerera ku zokonzekera zawo ndipo akufunabe mapointsi ambiri kuti athere pabwino.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi okwana 30 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligi.
"NGATI TISUNGE TIMU IYI TIDZACHITA BWINO KWAMBIRI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Wilson Chidati, wati timu yake imachita kukonzedwa chaka ndi chaka koma padakali panopa amanga timu yabwino yomwe ngati atayisunge idzachita bwino kwambiri chaka cha mawa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi FCB Nyasa Big Bullets 0-0 pa bwalo la Civo komabe atuluka mu mpikisano wa Airtel Top 8 poti anagonja 2-0 mu masewero oyamba ku Blantyre.
Iye anati, "Anali masewero abwino kwambiri, tinabwera tikutsalira nde timafuna kuti mwina tipange zinthu mofulumira kwambiri koma zatikanika komabe timuyi timakonza chaka ndi chaka ngati tingayisunge ndi mmene tikusewereramo ndekuti tidzakhala ndi timu yabwino."
Iye anatinso chidwi tsopano chapita pa masewero awo otsatira omwe akumane ndi timu ya Silver Strikers ndipo akonzeka bwino kuti adzachite bwino.
Zateremu timuyi tsopano yatuluka mu mpikisanowu kachiwiri ndi timu yomweyi ya Bullets yomwe inawatuluts
"OYIMBIRA ATIKANIRA CHIGOLI CHABWINO" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati oyimbira samayenera kuwakanira chigoli chimene iwo anagoletsa mchigawo choyamba poti chinali chabwinobwino pomwe chikanakhala chokhacho cha mmasewero omwe amasewera ndi MAFCO.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Chitowe ndipo wati timu yake inayesetsa kuti apeze chigoli koma ndi chimene chakanidwacho.
"Anali masewero ovuta kwambiri koma sindikudziwa maso a anzathu oyimbira poti tinapeza chigoli chabwinobwino koma iwo mkuona kwawo anachikana koma anali masewero ovuta kwambiri, ofunika mphamvu komanso ndi kutentha kwa kunoko masewero anatenthadi." Anatero Bunya.
Iye wati akufunitsitsa kuti timu yake ipezeko chipambano koyenda poti akachitako bwino ndekuti afanana mphamvu koma malingana ndi pomwe ali akuyenera azipambana.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe ili ndi mapointsi 25 pa masewero 22 omwe yasewera.
Man city
Kb
2020/21
"TIKUPITA KU MCHINJI KUKATENGA MAPOINTSI" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati akupita ku Mchinji kukakumana ndi timu yabwino kwambiri yomwenso ikuchita bwino kwambiri mu ligi koma akufunitsitsa kuti akapambane mmasewero awo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Creck Sporting Club pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji loweruka ndipo wati sakufuna zambiri koma kukatengako chipambano nkumabwera.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti tikukumana ndi timu yabwino kwambiri yomwe ikuchita bwino mu ligi ukaona nambala yomwe ali sikuti ndi poyipa kwambiri ndipo sikuti ndi yogwera koma tikupita ku Mchinji kuti tikatenge ma points atatu." Anatero Mponda.
Iye wati timu yake ikuchokera kopambana ndi timu ya Blue Eagles mu Castel Challenge Cup ndipo zimenezi ziwapatsa mphamvu kuti akayesetse kuti akapambane mmasewerowa.
Silver ikadali pa nambala yoyamba mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 49 pa masewero 21 omwe yasewera mu ligi.
Zosayenda
"TIZIMENYERE NKHONDO TOKHA" - KAFOTEKA
Mphunzitsi watimu ya FOMO, Elvis Kafoteka, wati timu yake ikuyenera kuonetsetsa kuti ikutolera mapointsi ochuluka pa masewero awo kuti izimenyere nkhondo posayang'ana kuti matimu ena akuchita motani.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Moyale Barracks pa bwalo la Mzuzu loweruka ndipo wati aonetsetsa kuchita chilichonse kuti apeze chipambano pa masewerowa.
"Akhala masewero ovuta Moyale ndi timu yabwino kwambiri koma ifeyo tikuyenera kuikapo mtima pofuna kuona kuti mapointsi amenewa akufunikira kwambiri kwa ifeyo osati iwowa nde tikayesetsa." Anatero Kafoteka.
Iye wati timu yake ikhonza kupambana masewerowa angakhale kuti Moyale ili pa khomo ndipo ati sakuyang'ana kuti matimu ena ayamba kuchita bwino koma kuti azimenyere nkhondo.
FOMO FC ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe ili ndi mapointsi 22 pa masewero 22 omwe yasewera mu ligi.
FAM YALANGA KAUNDA, THULU
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi lapereka chilango kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, kuti asapangenso za masewero zilizonse kwa miyezi kuyambira mwezi uno.
Izi zikudza malingana ndi zomwe mphunzitsiyu anachita pomwe timu yake imakumana ndi Blue Eagles mu chikho cha FDH Bank mmasewero omwe anagonja 2-0 pomwe sanakhutire ndi ziganizo za oyimbira.
Kupatula kusapezeka miyezi imeneyi, iyenso wauzidwa kuti alipire ndalama yokwana K500,000 kamba Ka milanduyi.
Ndipo wotseka kumbuyo kutimu yakeyi, Pilirani Thulu, naye wauzidwa kuti asasewere kwa chaka chimodzi kamba koti anagwira katundu wa oyimbira mmalo obisika pa masewero omwewa.
Zateremu Oscar Kaunda adzayambanso ntchito yake pa 18 June 2025 pomwe Thulu adzayamba pa 18 October 2025.
BREAKING NEWS:
The Super League of Malawi has handed a six-match ban to three Mafco FC players, Vitumbiko Phiri, Christopher Mikuwa and Blessings Chanding'ana for assaulting FCB Nyasa Big Bullets player, Wongani Lungu during their game in the TNM Super League.
The League's governing body has also slapped Mafco FC with a MK1 Million fine for bringing the game of football into disrepute and they have been given the chance to appeal against the Verdict in the next 48 hours.
Ibongese
Iponga win
Iponga 1οΌ2 Chitipa White Movers
"OLO MWANA WINA MNYUMBA AMAKHALA OBALALIKA KOMA SATAYIDWA" - MABEDI
Mphunzitsi watimu ya Malawi, Patrick Mabedi, wapempha masapota atimu ya dzikoyi kuti asawayang'anire kumbali koma apite akawonere masewero awo pomwe akukumana ndi Senegal masanawa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa pomwe amatsilizitsa zokonzekera ndipo wati timu yawo yagwirizana kuti akagonjetse Senegal mwa njira iliyonse pofuna kubwenza ngongole ya a Malawi onse.
"Angakhale pa khomo poti makhalidwe ake ndi abwino pamakhala mwana mmodzi oti khalidwe lake ndi lotayika komabe tikupempha kuti anthu asatitaye koma abwere mwaunyinji, tili ndi ngongole yawo ndipo tikabwenza lero." Anatero Mabedi.
Iye wati lero pokhala tsiku la anakubala, akuyenera kuti akometse tsikuli ndipo wati mwanjira iliyonse apeza chipambano ndipo akumvetsetsa mkwiyo wa amalawi komanso zomwe akumayankhula akumva.
Malawi ili ndi kamwayi kochepetsetsa komwe kakhonza kuwatengera ku African Cup of Nations ya chaka cha mawa ndipo ngati agonje kap
LOW FITNESS LEVELS OF LOCALS WORRIES MABEDI
Flames coach, Patrick Mabedi, says much needs to be done in our local league as most players in the league have their fitness levels very low leading to failure to much on in 90 minutes.
He said this ahead of the team's match against Senegal at the Bingu National Stadium on Tuesday afternoon and said most goals which Senegal scored on Friday last week were because of tiredness of the players.
He said, "I think we have more to do in our league as many locals are struggling with fitness which is worrisome, you can see most goals were scored in 70 minutes when most players were tired and they failed to cover up the defense when Senegal attacked so it's because the levels are down."
Meanwhile, Mabedi highlighted the need to get a win in the match as most Malawians are not pleased with the team's Current results.
Flames anchor their group with no point from three games whereas Burkina Faso have already qualified with Senegal on second.
Log table thumbs up srfl latest
"OLO PABWERE WINA NGATI SITIKONZA MAVUTO TIZIDZALUZABE" - MABEDI
Mphunzitsi watimu ya Malawi, Patrick Mabedi, wati pali mavuto ochuluka kwambiri omwe akupangitsa kuti timuyi isamachite bwino ndipo kumuchotsa iyeyo ndi kubweretsa wina sizingasinthe kanthu ngati mavutowa sakonzedwa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Senegal lachiwiri pa bwalo la Bingu ndipo wati ngati dziko tikuyenera kugwirana manja kuti mpira wathu uyende bwino komabe poti mtsogoleri ndi iyeyo akuvomera zonse zomwe anthu akumamunenera.
Iye wati akumva kuwawa kwambiri kuti timuyi sikuchita bwino chimodzimodzi osewera ndipo agwirizana kuti mtsiku la mawa adzakometse tsiku la anakubala ndi chipambano.
"Tikuyenera kuchita bwino mwanjira iliyonse chifukwa sitinachite bwino masewero apita aja nde apa tili kwathu komanso tsiku lokumbukira anakubala nde tikuyenera kuti anthu akamasangalala zinazi, ifenso tichite bwino." Anatero Mabedi.
Iye wati sakutekeseka pa ntchito yake pa chiopsezo kuti mwina ntchito yake ikhonza kutha chifukwa wati sizachilendo kuti ntchito yatha koma iye apitilirabe kugwira ntchito.
Iye watinso ali ndi ngongole kwa amalawi kamba koti samachita bwino ndipo mtsiku la mawa akukabwenza ngongole imeneyi.
Padakali panopa, timuyi yalephera kupeza chipambano chilichonse pa masewero awo mu gululi ndipo ali pansi penipeni opanda angakhale point imodzi ndipo ngati angagonje mawa akhala kuti akanikiratu ku mpikisanowu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Silver strickers
CAF STATEMENT ON NIGERIA/LIBYA MATCH
CAF views the disturbing and unacceptable experiences of the Nigerian National Football Team (ββSuper Eaglesββ) at an airport in Libya in a very serious light.
CAF has been in contact with the Libyan and Nigerian authorities after it had been informed that the Nigerian National Football Team and their technical team were stranded in disturbing conditions for several hours at an airport that they were allegedly instructed to land by the Libyan authorities.
The matter has been referred to the CAF Disciplinary Board for investigation and appropriate action will be taken against those who violated the CAF Statutes and Regulations.
NEWS
Nigeria Super Eagles and all their officials are now boarding the plane to get back home to Nigeria from Libya.
Despite Patrice Motsepe appeal for Nigeria to stay and honour the game, the NFF refused and the game will not go ahead tomorrow as scheduled.
The Nigeria Football Federation has decided to pull the Super Eagles out of Tuesdayβs 2025 Africa Cup of Nations qualifier against Libya.
This follows a frustrating 12-hour ordeal at Al Abraq International Airport in Libya, where the team has been stranded since their arrival on Sunday afternoon.
The PUNCH reports that the Nigerian delegation was en route to Benghazi for the crucial qualifier when their chartered aircraft was dangerously diverted mid-flight to Al Abraq, a small airport typically reserved for hajj operations....
SILVER, WANDERERS RETURN TO ACT ON THURSDAY
Elite League sides, Silver Strikers and Mighty Mukuru Wanderers will play their round of 64 matches in the Castel Challenge Cup two days after their players returning from the National team assignment as per Football Association of Malawi communication.
This comes after the Association released the dates for the remaining fixtures to complete the teams that have booked their place in the round of 32.
The Bankers will have to swear in order to stage a revenge on Blue Eagles which knocked them out of the FDH Bank Cup enroute to win it in August while the Nomads will play Nsuwadzi FC from Mulanje both matches on Thursday, 17th of October 2024.
Meanwhile, these will be last fixtures in the round of 64 as two fixtures will be played on Tuesday and one on Wednesday. Here are the fixtures:
TUESDAY, 15 OCTOBER 2024
β’Iponga FC vs Chitipa White Rovers @ Karonga Stadium
β’Maonga (Thyolo) vs Umodzi FC (Nsanje) @ Mpira Stadium
WEDNESDAY, 16 OCTOBER
0-1