"SITIMAMENYA NDI CRECK KOMA GULU" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati zotsatira za masewero atimu yake ndi Creck Sporting Club sizabwino poti amafunitsitsa atapambana koma vuto amamenya ndi osewera odutsa khumi ndi mmodzi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati chigoli chachiwiri cha anzawowa sichinali chabwinobwino..
"Anali masewero abwino kwambiri tasewera bwino ku mbali yathu koma zotsatira nde sizabwino komabe lero sitinasewere ndi osewera 11 koma timasewera ndi ambiti, chigoli chachiwiri chawo chija kaya poti kuona kwawo koma kumbali yanga sichimayenera kuloledwa." Anatero Mponda.
Iye wati timu yake ili ndi masewero aakulu patsogolo pawo ndi timu ya Civil Service United ndipo ndi mmene asewerera ndi Blue Eagles komanso Creck akukhulupilira kuti akachita bwino.
Timuyi ikadali pamwamba pomwe ili ndi mapointsi okwana 50 pa masewero 22 omwe asewera.
MUTUMIZILE KU 0981511741
Tumizilani pa 0981511741
Takutumizirani nonse awiri 👏👏
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores