"OLO PABWERE WINA NGATI SITIKONZA MAVUTO TIZIDZALUZABE" - MABEDI
Mphunzitsi watimu ya Malawi, Patrick Mabedi, wati pali mavuto ochuluka kwambiri omwe akupangitsa kuti timuyi isamachite bwino ndipo kumuchotsa iyeyo ndi kubweretsa wina sizingasinthe kanthu ngati mavutowa sakonzedwa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Senegal lachiwiri pa bwalo la Bingu ndipo wati ngati dziko tikuyenera kugwirana manja kuti mpira wathu uyende bwino komabe poti mtsogoleri ndi iyeyo akuvomera zonse zomwe anthu akumamunenera.
Iye wati akumva kuwawa kwambiri kuti timuyi sikuchita bwino chimodzimodzi osewera ndipo agwirizana kuti mtsiku la mawa adzakometse tsiku la anakubala ndi chipambano.
"Tikuyenera kuchita bwino mwanjira iliyonse chifukwa sitinachite bwino masewero apita aja nde apa tili kwathu komanso tsiku lokumbukira anakubala nde tikuyenera kuti anthu akamasangalala zinazi, ifenso tichite bwino." Anatero Mabedi.
Iye wati sakutekeseka pa ntchito yake pa chiopsezo kuti mwina ntchito yake ikhonza kutha chifukwa wati sizachilendo kuti ntchito yatha koma iye apitilirabe kugwira ntchito.
Iye watinso ali ndi ngongole kwa amalawi kamba koti samachita bwino ndipo mtsiku la mawa akukabwenza ngongole imeneyi.
Padakali panopa, timuyi yalephera kupeza chipambano chilichonse pa masewero awo mu gululi ndipo ali pansi penipeni opanda angakhale point imodzi ndipo ngati angagonje mawa akhala kuti akanikiratu ku mpikisanowu.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores