"MAFCO TSOPANO ILI BWINO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO FC, Pritchard Mwansa, wayamikira osewera atimuyi kamba ka kuzipereka kwawo kuti kukuthandiza timuyi kuchita bwino kwambiri mmasewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 2-0 ndi Ekwendeni Hammers ndipo wati tsopano timu ya MAFCO ili bwino kwambiri.
"Ndife wosangalala kamba ka chipambanochi, anali masewero ofunikira kwambiri poti ligi yavuta pa log table koma anyamata akuchita bwino, mmasewero 5 apitawa tachita bwino mwina ndi mmene ligi ilili sizophweka kupambana masewero 4-5 nde tiwathokoze." Mwansa anafotokoza.
Timuyi yachoka pa nambala 12 ndipo yafika pa nambala 8 ndi mapointsi 31 pa masewero 24 omwe iyo yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores